LA MULUNGU LA 23 PA CHAKA (CYCLE C)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA LUNTHA; LUNTHA 09: 13 – 18. (Ndani angathe kuzindikira zimene Ambuye akufuna?)
Kodi ndani angathe kudziwa maganizo a Mulungu? Ndani angathe kuzindikira zimene Ambuye akufuna? Nzeru za anthu nzoperewera, zolinga zathu nzotha kulephera. Chifukwa thupi lodzafali limalemetsa mtima, nyumba yake yadothiyi imavuta mtima woganiza zambiri. Nkwapatali kale kwa ife kulota zimene zili pansi pano, ndipo timachita kuvutikira kuti timvetse ngakhale zimene zili pafupi nafe. Nanji tsono zimene zili kumwamba, angazitulukire ndani? Ndani angathe kudziwa kufuna kwanu Ambuye, mutapanda kumupatsa luntha, kapena kumutumizira mzimu wanu woyera kuchokera kumwamba? Motero njira za anthu a pansi pano zidalungamitsidwa, anthu adaphunzira zimene zimakukomerani, ndipo adapulumuka chifukwa cha luntha.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 03 – 06, 12 – 14, 17.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Inu mumabwezera
anthu ku fumbi,
Ndipo mumati, “bwerani
inu ana a anthu.”
Pakuti zaka chikwi
chimodzi pamaso panu zili ngati dzulo chabe,
Kapena ngati
kamphindi chabe kausiku.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Inu mumachotsa
moyo wa anthu mwadzidzi,
Ali ngati
maloto, ali ngati udzu wongotsitsimuka m’mawa,
M’mamawamo
umatsitsimuka ndipo umakondwa,
Madzulo umafota
ndi kuuma.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Tsono
tiphunzitseni kuwerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru,
Lezani mtima, Inu
Chauta.
Nanga
mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni
chifundo atumiki anu.
Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Tidzazeni m’mawa
mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika,
Kuti tizikondwa
ndi kusangalala masiku athu onse.
Inu Ambuye,
mutikomere mtima, ndipo mudalitse ntchito zonse za manja athu.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA FILEMONI: FILEMONI 09 – 10: 12 – 17. (Udzakhale naye ngati mbale wokondedwa.)
Iwe Filemoni, chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m’ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu. Ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga mwa Khristu, amene ndidachita ngati kumubala m’ndende muno. Iyeyu ndi Onesimo. Ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, ndipo pakutero ndikuchita ngati kukutumizira mtima wanga womwe. Ndikadakonda kuti akhalebe ndi ine kuno, kuti azinditumikira m’malo mwako, pokhala ndili m’ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino. Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, kuwopa kuti ungandichitire chinthu chabwinochi mokakamizidwa, osati mwaufulu. Kapena Onesimo anangokusiya kanthawi pang’ono, kuti udzakhale naye nthawi zonse, osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati m’bale wokondeka. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu m’nzako ndiponso mkhristu m’nzako. Tsono ngati umati ndine bwenzi lako, umlandire iyeyu monga momwe ukadandilandilira ineyo.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – SALIMO 119: 135.
Alleluia, Alleluia – Yang’anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 14: 25 – 33. (Aliyense mwa inu atha kukhala wophunzira wanga pokhapokha atagulitsa chuma chake chonse.)
Chikhamu cha anthu chinkatsagana ndi Yesu. Tsono Iye adatembenuka nawauza kuti, “aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda ine kuposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe. Aliyense amene sasenza mtanda wake nkumanditsata, sangakhale wophunzira wanga. Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuwerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. Adzati, ‘mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’ Chimodzimodzinso kodi ndi Mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenya ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi awiri. Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali. Chonchonso aliyense mwa inu amene sasiya zonse zimene ali nazo, sangakhale ophunzira wanga.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment