LAMULUNGU LA 25 PACHAKA (CYCLE C)
“Nditani nacho chuma changa?”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI AMOSI; AMOSI 08: 04 – 07. (Imvani izi, inu amene mumapondereza osowa, amene mufuna kugula osauka ndi siliva.)
Amosi adati, “imvani izi, inu amene mumapondereza osowa, amene mufuna kuwononga anthu osauka a m’dzikomu. Inu mumazifunsa kuti, ‘kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzachitika liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndikukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama, kuti osauka tiwagule ndi siliva, amphawi tiwagule ndi nkhwawiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’” Chauta, Mulungu amene ana a Yakobe amamnyadira walumbira kuti, “Ndithudi, sindidzaiwala zochita zao zonse.”
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 113: 01 – 02, 04 – 08.
Tamandani Chauta, amene amatulutsa ku dzala anthu osowa.
Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake,
Tamandani dzina la Chauta. Yamikani Chauta.
Dzina la Chauta litamandike,
Kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Chauta, amene amatulutsa ku dzala anthu osowa.
Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse,
Ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga,
Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu,
Amene akukhala kumwamba, wochita kuweramira pansi,
Poyang’ana mlengalenga ndi dziko lapansi.
Tamandani Chauta, amene amatulutsa ku dzala anthu osowa.
Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi,
Ndipo amatulutsa ku dzala anthu osowa,
Amawakhazika pamodzi ndi mafumu,
Mafumu a Chauta.
Tamandani Chauta, amene amatulutsa ku dzala anthu osowa.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 01 TIMOTEO 02: 01 – 08. (Pakhale mapemphero opempherera anthu kwa Mulungu, amene afuna kuti anthu onse apulumuke.)
Abale, choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Mudziwapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza. Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, mpulumutsi wathu. Iye amafuna kuti anthu onse apulumuke ndipo kuti adziwe choona. Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu. Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthawi yake. Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu amitundu ina mau a chikhulupiliro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona. Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira Ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 02 Akorinto 08:09
Alleluia, Alleluia – Ambuye athu Yesu Khristu anali wolemera, koma adakhala mmphawi chifukwa cha inu, kuti ndi umphawi wakewo inu mukhale olemera. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 16: 01 – 13/ [16: 10 – 13] (Simungathe kutumikira onse awiri, Mulungu ndi chuma.)
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “panali munthu wina wachuma amene anali ndi kapitao wake. Anthu adadzamneneza kapitawoyo kuti akumwaza chuma cha mbuye wake. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso kukundichititsa manyazi. Chabwino, tsopano ndadziwa choti ndichite, kuti anthu akandilandire ku nyumba zao, ukapitao ukandithera.’ Motero adaitana angongole a mbuye wake mmodzimmodzi. Adafunsa woyamba kuti, ‘kodi uli ndi ngongole yotani kwa mbuye wanga?’ Iye adati, ‘mafuta amuyeso wokwanira Mitsuko makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘nayi kalata yako ya ngongole, khala pansi msanga, ungolembapo Mitsuko makumi asanu.’ Adafunsanso wina kuti, ‘nanga iwe, ngongole yako ndiyotani?’ iye adati, ‘tirigu wamuyeso wokwanira matumba makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘nayi kalata yako ya ngongole, ungolembapo matumba makumi asanu ndi atatu.’ Apo mbuye wa kapitao wonyenga uja adamuyamikira chifukwa cha kuchenjera kwake. Pajatu pokhala ndi anzao, anthu okonda zapansi pano ngochenjera koposa anthu okhala m’kuwala kwa Mulungu.”’ Yesu popitiriza mau adati, “ndipo ine ndikukuuzani kuti mudzipezere abwenzi achuma chonyengachi. Apo chumacho chikadzakutherani, Mulungu adzakulandirani ku nyumba zamuyaya. Wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ngokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing’ono, amanyenganso pa zazikulu. Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu? Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana awiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse awiri, Mulungu ndi chuma.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment