LAMULUNGU LA 26 PACHAKA (CYCLE C)
“Kalanga ine! Ndikadadziwa!”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI AMOSI; AMOSI 06: 1a, 04 – 07. (Inu anthu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu nkumangoimba azeze, mudatsogoza ndinu kupita ku ukapolo.)
Tsoka kwa inu amene mumakhala mosateketseka ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya. Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Israeli, inu amene anthu onse amafika kwanu. Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga yanjovu, inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu, nkumachita phwando la nyama la anaankhosa ndi anaang’ombe onenepa. Ntchito nkumangoimba azeze ngati Davide, ndikumangopeka nyimbo zoimbira pa zingw’enyengw’enye. Tsoka kwa inu amene mumamwera vinyo m’zipanda zodzadza, inu amene mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa dziko la Yosefe. Nchifukwa chake mudzatsogola ndinu kupita ku ukapolo, ndipo maphwando ndi zikondwerero zidzakutherani.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 06 – 10.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Amasunga malonjezo ake nthawi zonse,
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,
Amawapatsa chakudya anthu anjala,
Chauta amamasula am’ndende.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,
Chauta amakweza anthu otsitsidwa,
Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,
Chauta amateteza alendo.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wa wamasiye,
Koma njira za anthu oipa amazipotoza,
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 01 TIMOTEO 06: 11 – 16. (Utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso.)
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri. Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene popereka umboni pamaso pa Ponsio Pilato, adaanena zoona zenizeni. Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso. Pa nthawi yake Mulungu adzamuonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse. Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m’kuwala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuona, palibenso amene angathe kumuona. Kwa iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 02 Akorinto 08: 09.
Alleluia, Alleluia –Ambuye athu Yesu Khristu anali wolemera, koma adakhala mmphawi chifukwa cha inu, kuti umphawi wakewo inu mukhale olemera. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 16: 19 – 31. (Kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zowawa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri.)
Yesu adauza Afarisi kuti, “panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala za mtengo wapatali, ndipo ankasangalala ndikudyerera masiku onse. Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankangogona pakhomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m’thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma sipokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. Munthu osauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m’manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m’manda. Pamene ankazunzika ku malo a anthu akufa, wachuma uja adayang’ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro pambali pakepa. Pamenepo adaanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m’madzi kuti adzidziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m’moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zowawa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndipo pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kubwera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuworokera kuno.’ Apo wachuma uja adati, ‘ndipotu ndikukupemphani Atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akawachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere za m’menemo.’ Iye adati, ‘iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.”’
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295