LA MULUNGU LA 22 PA CHAKA (CYCLE C)
“Tipewe khalidwe lakunyada ndi lakudzikonda.”
MAU
WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPHUNZITSI; MPHUNZITSI 03: 17 –
19, 28 – 29. (Udzichepetse, ukatero udzapeza kuyanja pamaso pa Ambuye.)
Mwana wanga, ukhale wodekha pa zonse zimene umachita, ndipo anthu okomera Ambuye adzakukonda. Ngati ndiwe wotchuka kwambiri, udzichepetse, ukatero udzapeza kuyanja pamaso pa Ambuye. Pali anthu ambiri otchuka ndi amphamvu, koma Ambuye amaulula zinsinsi zao kwa anthu odzichepetsa. Tsoka likagwera onyada, palibe mankhwala, pakuti kuipa kumakhala kutazika mizu mwa iye. Munthu wochenjera amalingalira bwino fanizo, munthu wanzeru amafunitsitsa kukhala ndi makutu atcheru.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO: 68: 04 – 07, 10 – 11.
Mwakukoma mtima kwanu, Inu Chauta, mwakonza malo okhala anthu ovutika.
Anthu anu
Mulungu, akondwere,
Asangalale
pamaso panu,
Inde, asekere
ndi chimwemwe,
Muimbireni Mulungu,
imbani nyimbo zotamanda dzina lake.
Mwakukoma mtima
kwanu, Inu Chauta, mwakonza malo okhala anthu ovutika.
Atate a ana
amasiye ndiponso Mtetezi wa azimai amasiye,
Ndi Mulungu
amene amakhala m’malo ake oyera,
Anthu osiyidwa,
Mulungu amawapatsa malo okhalamo,
Am’ndende
amawatulutsa kuti akhale pa ufulu.
Mwakukoma mtima
kwanu, Inu Chauta, mwakonza malo okhala anthu ovutika.
Inu Mulungu,
mudagwetsa mvula yokwanira pa dziko,
Mudalimbitsanso
dziko, pamene lidaali lofooka,
Anthu anu
adapezamo malo okhala,
Inu Mulungu,
mudapatsa anthu osauka zao mwa ubwino wanu.
Mwakukoma mtima
kwanu, Inu Chauta, mwakonza malo okhala anthu ovutika.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOLEMBERA AHEBERI; AHEBERI 12: 18 – 19, 22 – 24a. (Inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo.)
Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asawamvenso konse. Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo, ndiye kuti Yerusalemu wa Kumwamba, m’mene muli Angelo osawerengeka. Mwafika kuchikondwelero kumene kwasonkhana ana oyamba a Mulungu, amene maina ao adalembedwa Kumwamba. Mwafika kwa Mulungu, mweruzi wa anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama, amene Mulungu wawasandutsa angwiro kwenikweni. Mwafika kwa Yesu, Nkhoswe yokonza za chipangano chatsopano, ndiponso mwafika ku magazi okhetsedwa, amene akutilonjeza zinthu zabwino koposa m’mene magazi a Abele ankachitira.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – MATEYO 11: 29ab
Alleluia, Alleluia – Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 14: 01, 07 – 14. (Aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.)
Pa tsiku lina la sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m’gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa. Yesu adaaona kuti anthu amene adaaitanidwa kudzadya nao ankadzisankhira malo aulemu. Tsono adawaphera fanizo, adati, “wina akakuitana ku phwando la ukwati, usamakhala pa malo aulemu ai, chifukwa mwina kapena adaitananso wina waulemu kuposa iwe. Ndiye iye uja amene adaitana awiri nonsenu nkudzakuuza kuti, ‘pepani, patsani awa malowa.’ Apo iweyo udzachita manyazi pokakhala pa malo otsika. Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘bwezi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.” Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphoto yako. Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphawi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295