LAMULUNGU LACHINAYI MU NYENGO YA PASAKA - CYCLE C
(Nkhosa zanga zimamva mau anga.)
MAWU WOYAMBA: MAWU A M'BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 13: 14, 43 – 52. (Ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja.)
Kuchokera ku Perga iwo adapitilira nakafika ku Antiokeya m’dera la Pisidiya. Patsiku la Sabata adalowa m’nyumba yamapemphero ya a Yuda, nakhala pansi. Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu Ina otembenuka nkumatsata zachiyuda, adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Awiriwa adalankhula ndi anthu aja, nawapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adawachitira mwa kukoma mtima kwake. Pa tsiku la sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye. Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo amkanena, ndipo adamchita chipongwe. Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwawakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu a kunja. Paja Ambuye adatilamula kuti, ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ Pamene anthu amitundu Ina ija adamva zimenezi, anakondwa, nayamikira mawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adawasankha kuti alandira moyo Wosatha, adakhulupilira. Mau a Ambuye adafikira m’dziko monse muja. Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, nawapirikitsa m’dziko mwaomo. Koma iwo adasasa fumbi la ku mapazi kwao mowatsutsa, napita ku Ikonia. Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu woyera ndipo adakhala ndi Chimwemwe chachikulu.
Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 100: 01 – 02, 03, 05.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse!
Tumikirani Chauta mosangalala.
Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Dziwani kuti Chauta ndiye Mulungu.
Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake,
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Paja Iye ndi wabwino.
Chikondi chake nchamuyaya,
Kukhulupirika kwake nkosatha.
Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO; CHIVUMBULUTSO 07: 09, 14b – 17. (Mwanawankhosa uja adzakhala Mbusa wao ndipo
adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.)
Ine, Yohane, nditayang’ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osawerengeka. Anthuwo anali ochokera m’mitundu yonse ya anthu, ndi m’mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m’manja. Ine ndidati, Mbuyanga, mukudziwa ndinu. Ndipo iye adandiwuza kuti, amenewa ndi amene adapambana m’masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa. Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m’Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adakhala ngati hema lao lowateteza. Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaombedwanso ndi dzuwa kapena kusauka ndi kutentha. Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse m'maso.
Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia!! Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo
izozo Ineyo zimandidziwa. Alleluia, Alleluia!!
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 10: 27 – 30. (Ndimazipatsa moyo wosatha nkhosa zanga.)
Yesu anati, “Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira. Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m’manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo
palibe amene angathe kuzilanda m’manja mwao. Ine ndi Atate ndife amodzi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment