LAMULUNGU
LA 03 LA PASAKA - CYCLE C
(Yesu apitiriza kudzionetsa Kwa ophunzira ake.)
MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 05: 27 – 32, 40 – 41. (Mboni a zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera.)
Mkulu wa ansembe onse adayamba kuwafunsa Apositoli mafunso.
Adati, “paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m’dzina la Yesu,
koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna
kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.” Koma Petro ndi atumwi enawo adati,
“tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu. Mulungu wa makolo athu
adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda.
Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi.
Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao
akhululukidwe. Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu
adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera lye.” Pambuyo pake, abwalowo
adawaitana atumwi aja. Adawakwapula, nawaletsa kuti asalankhulenso m’dzina la
Yesu, kenaka adawalola kuti apite. Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti
Mulungu wawawerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu.
Mawu a
Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30: 02. 04 – 06. 11 – 13.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Simudalole kuti adani anga
akondwere,
Pakuti mwanditulutsa m'dzenje la
imfa,
Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko
la akufa,
Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta,
Inu anthu ake oyera mtima,
Mumthokoze chifukwa cha dzina lake
loyera,
Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe,
Koma kukoma mtima kwake nkwa moyo
wonse.
Misozi ingachezere kugwa usiku,
M’mawa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.
Imvani, Inu Chauta, ndipo
mundikomere mtima.
Inu Chauta, mukhale mthandizi
wanga.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti
kukhale kuvina,
Mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta,
pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO;
CHIVUMBULUTSO 05: 11 – 14. (Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera
kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.)
Pambuyo pake nditayang’ana ndidaona namtindi wa angelo zikwi-zikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja. Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko. Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cha m’nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire Chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.” Apo zamoyo zinai zija zidati, “Amen.” Ndipo akuluakulu aja adadzigwetsa pansi mowerama, napembedza.
Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia!! Ambuye wauka: Iwo amene analenga zonse ndipo chifundo chawo anagawira anthu onse. Alleluia, Alleluia!!
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 21: 01 – 19 (Yesu adadza natenga buledi uja nkuwapatsa. Adateronso ndi nsomba Zija.)
Pambuyo pake Yesu adadziwonetsanso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiasi. Adadziwonetsa motere: Simoni Petro, Tomasi (wotchedwa Didimo), Natanaele wochokera ku mudzi wa Kana m’dera la Galilea, ana aja a Zebedeo, ndiponso ophunzira ena awiri, anali pamodzi. Simoni Petro adawauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakalowa m’chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu. Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu. Tsono Iye adawafunsa kuti, “Kodi anzathu, mwaphako kanthu ngati?” Iwo adati, “Ai ndithu, tabwera chabe.” Yesu adawauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m’nyanja. Koma ophunzira ena aja adadza ndi chombo ku mtunda akukoka khoka lodzaza ndi nsomba. Sanali kutali ndi mtunda, koma pafupi, ngati mamita 90. Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi. Yesu adawauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.” Apo Simoni Petro adalowa m’chombo muja nakokera khoka lija ku mtunda, lodzaza ndi nsomba zazikulu zokwanira 153. Ngakhale nsombazo zinali zochuluka chotero, khokalo silidang'ambike. Yesu adawauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa phunzirawo panalibe ndi m’modzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye. Yesu adadza natenga buledi uja nkuwapatsa. Adateronso ndi nsomba zija. Aka nkachitatu kuti Yesu aonekere ophunzira ake lye atauka kwa akufa. Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m’mene amandikondera awa?” Iye adati. “Inde Ambuye, mukudziwa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiwiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziwa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Weta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziwa zonse. Mukudziwa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga. Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.” (Yesu adanena zimenezi pofuna kuwadziwitsa za m’mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, "Unditsate.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook:
https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment