Saturday, April 30, 2022

 

LAMULUNGU LA 03 LA PASAKA - CYCLE C

(Yesu apitiriza kudzionetsa Kwa ophunzira ake.)

MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 05: 27 – 32, 40 – 41. (Mboni a zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera.)

Mkulu wa ansembe onse adayamba kuwafunsa Apositoli mafunso. Adati, “paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m’dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.” Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu. Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda. Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe. Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera lye.” Pambuyo pake, abwalowo adawaitana atumwi aja. Adawakwapula, nawaletsa kuti asalankhulenso m’dzina la Yesu, kenaka adawalola kuti apite. Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti Mulungu wawawerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu.

Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30: 02. 04 – 06. 11 – 13.

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

Simudalole kuti adani anga akondwere,

Pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa,

Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko la akufa,

Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.

Imbani nyimbo zotamanda Chauta,

Inu anthu ake oyera mtima,

Mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera,

Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe,

Koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse.

Misozi ingachezere kugwa usiku,

M’mawa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.

Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima.

Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga.

Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina,

Mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa.

 

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO; CHIVUMBULUTSO 05: 11 – 14. (Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.)

Pambuyo pake nditayang’ana ndidaona namtindi wa angelo zikwi-zikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja. Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko. Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cha m’nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire Chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.” Apo zamoyo zinai zija zidati, “Amen.” Ndipo akuluakulu aja adadzigwetsa pansi mowerama, napembedza.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO

Alleluia, Alleluia!! Ambuye wauka: Iwo amene analenga zonse ndipo chifundo chawo anagawira anthu onse. Alleluia, Alleluia!!

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 21: 01 – 19 (Yesu adadza natenga buledi uja nkuwapatsa. Adateronso ndi nsomba Zija.)

Pambuyo pake Yesu adadziwonetsanso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiasi. Adadziwonetsa motere: Simoni Petro, Tomasi (wotchedwa Didimo), Natanaele wochokera ku mudzi wa Kana m’dera la Galilea, ana aja a Zebedeo, ndiponso ophunzira ena awiri, anali pamodzi. Simoni Petro adawauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakalowa m’chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu. Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu. Tsono Iye adawafunsa kuti, “Kodi anzathu, mwaphako kanthu ngati?” Iwo adati, “Ai ndithu, tabwera chabe.” Yesu adawauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m’nyanja. Koma ophunzira ena aja adadza ndi chombo ku mtunda akukoka khoka lodzaza ndi nsomba. Sanali kutali ndi mtunda, koma pafupi, ngati mamita 90. Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi. Yesu adawauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.” Apo Simoni Petro adalowa m’chombo muja nakokera khoka lija ku mtunda, lodzaza ndi nsomba zazikulu zokwanira 153. Ngakhale nsombazo zinali zochuluka chotero, khokalo silidang'ambike. Yesu adawauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa phunzirawo panalibe ndi m’modzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye. Yesu adadza natenga buledi uja nkuwapatsa. Adateronso ndi nsomba zija. Aka nkachitatu kuti Yesu aonekere ophunzira ake lye atauka kwa akufa. Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m’mene amandikondera awa?” Iye adati. “Inde Ambuye, mukudziwa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiwiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziwa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Weta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziwa zonse. Mukudziwa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga. Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.” (Yesu adanena zimenezi pofuna kuwadziwitsa za m’mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, "Unditsate.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, April 23, 2022


LAMULUNGU LA 02 MU NYENGO PASAKA (LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE (Iwo adakondwera kwambiri poona Ambuye.)

MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 05: 12 – 16 (Anthu okhulupirira Ambuye, amuna ndi akazi, ankachulukirachulukira.)

Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m’Khonde la Solomoni. Mwa anthu enawo panalibe ndi m’modzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankawatama. Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m’miseu ya mumzinda, nkumawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiwafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yowaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.

Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 02 – 04. 22 – 27.

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

Aisraele anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.

Banja la Aroni linene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.

Anthu oopa Chauta anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga.

Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta,

Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino.

Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta.

Tikufunirani madalitso ochokera m'Nyumba ya Chauta.

Chauta ndi Mulungu, ndipo watipatsa kuwala.

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 01: 09 – 13. 17 – 19 (Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya.)

Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m’kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Pa tsiku la Ambuye ndidaagwidwa ndi Mzimu Woyera, nkumva kumbuyo kwanga liwu la mphamvu ngati kulira kwa lipenga. Liwulo lidati, “zimene ukuwonazi, uzilembe m'buku ndipo ulitumize kwa mipingo isanu ndi iwiri iyi: wa ku Efeso, wa ku Smirina, wa ku Pergamo, wa ku Tiatira, wa ku Sardi, wa ku Filadelfiya ndi wa ku Laodikea.” Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. Pakati pake pa ndodo za nyalezo ndidaona wina wooneka ngati mwana wa munthu. Anali atavala mkanjo wautali, atamangira lamba wagolide pa chifuwa. Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati: “Usaope. Woyamba ndiponso wotsiriza ndine. Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine. Lemba tsono zimene waziona, ndiye kuti zimene zikuchitika tsopano ndi zimene zidzachitike bwino lino.”

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 20: 29.

Alleluia, Alleluia!! Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. Alleluia, Alleluia!!


MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 19 – 31 (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera.)

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupilire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m'nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembwedwa kuti mukhulupilire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Sunday, April 17, 2022

LAMULUNGU LA PASAKA – CYCLE C

“Yesu Khristu ndiye moyo wathu.”

 

MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 10: 34, 37 – 43. (Adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.)

 

Petro adayamba kulankhula, adati, "Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera. Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa. Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe. Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”

 

Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 01 – 02, 16 – 17, 22 – 23.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. / Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

ndipo chikondi chake nchamuyaya.

Aisraele anene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.”

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. / Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Dzanja lamanja la Chauta lapambana,

dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”

Sindidzafa, ndidzakhala moyo,

ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. / Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

womwewo wasanduka mwala wapangodya.

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. / Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE: AKOLOSE 03: 01 – 04 (Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.)

 

Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.

 

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO

 

Alleluia, Alleluia!!

 

Kankhosa kathu ka Pasaka ndiye Yesu Khristu amene waphedwa ngati nsembe. Tiyeni tsopano, tichite chikondwerero choyamikira Ambuye.

 

Alleluia, Alleluia!!

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 01 – 09 (Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.)

 

Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m’mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” Pamenepo Petro ndi wophunzira wina uja adatuluka napita ku manda. Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo. Simoni Petro atafika akumutsatira, adaloŵa m'mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, April 9, 2022

 


LAMULUNGU LA KANJEDZA (CHIYAMBI CHA MLUNGU WOYERA) CYCLE C

MTHENGA WABWINO (KU M’DIPITI): MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 19: 28 – 40 (Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye)

Yesu adatsogolera ophunzira ake kupita ku Yerusalemu. Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira awiri, nawauza kuti, “pitani m’mudzi mukuwonawo. Mukakangolowamo mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukam’masule, nkubwera naye kuno. Wina akakakufunsani kuti, ‘mukum’masuliranji?’ Mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito.”’ Awiriwo adapita, nakapezadi monga momwe Yesu adaawauzira. Pamene ankamasula mwanawabuluyo, eni ake adawafunsa kuti, “mukum’masuliranji, mwanawabuluyu?” Iwo adati, “Ambuye ali naye ntchito.” Tsono adapita naye kwa Yesu, nayamba kuyala zovala zao pa buluyo, nakwezapo Yesu. Pamene Yesu ankapita, anthu adamchitira ulemu pakuyala zovala zao mu mseu. Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. Adati, “ndi yodala Mfumu imene ilikudza m’dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti. “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuwa aleke zimenezi.” Iye adati, “ndikutitu iwowa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi?”

Mthenga wa Ambuye................. Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

PAMBUYO PA M’DIPITI.


MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 50: 04 – 07. (Sindidawabisire nkhope ondinyoza. Ndikudziwa kuti Chauta sadzandichititsa manyazi.)

Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziwe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M’mawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira. Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidawanyoze kapena kuwapandukira. Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidawabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwawo sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziwa kuti sadzandichititsa manyazi.

Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 22: 08 – 09, 17 – 18, 19 – 20, 23 – 24.

Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Onse ondiwona amandiseka,

Amandikwenzulira ndi kupukuta mitu two.

Amati, “unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse.

Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.”


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu.

Aboola manja anga ndi mapazi anga.

Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang’anitsitsa,

Akukondwera poona kuti ndikuvutika.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Agawana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere.

Koma Inu Chauta musakhale kutali.

Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu.

Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu.

Ndidzati, ‘Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye.

Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye,

inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.’


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 02: 06 – 11. (Ali munthu choncho adadzichepetsa, koma Mulungu adamkweza kopambana.)

Abale, Yesu Khristu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingama ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphawi wa kapolo, ndi kukhala munthu monga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza. Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 02: 08 – 09.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!

Ambuye, adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Nchifukwa chake chimene Mulungu adamkweza kopambana nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!


MTHENGA WABWINO: KUSAUKA KWA YESU KHRISTU AMBUYE ATHU MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 22: 14 –– 23:56

W. – Wowerenga.

Y. – Yesu.

M. – Munthu.

A. – Anthu ena.


1. YESU ADACHITA PHWANDO LA PASAKA NAPANGA UKARISTIA.

W. Nthawi itakwana, Yesu adakakhala podyera pamodzi ndi atumwi ake aja. Tsono adawauza kuti:

Y. Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Pasaka pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zowawa. Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Pasaka, mpaka Pasakayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.

W. Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu adati:

Y. Kwayani, imwani nonsenu. Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.

W. Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati:

Y. Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.

W. Atatha kudya, adawapatsanso chikho, nati:

Y. Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira. Koma ndithudi wondipereka kwa adani akudya nane pamodzi pompano. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.

W. Apo onse adayamba kumafunsana kuti:

A. Kodi ndani mwa ife angachite zotere?

W. Tsono ophunzira aja adayamba kutsutsana kuti:

A. Kodi mwa ife amati wamkulu ndani?

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amawaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira. Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira. Inu ndinu amene mwakhala ndi Ine pa masautso anga onse. Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu. Ndikadzalowa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukawalimbitse abale akowa.

W. Apo Petro adati:

M. Ambuye, ndili wokonzeka kupita nanu ku ndende, ngakhale kufa kumene.

W. Koma Yesu adamuyankha kuti:

Y. Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziwa.

W. Yesu adawafunsa kuti:

Y. Nthawi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasowapo kanthu?

W. Iwo adati:

A. Iyai.

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga. Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, “Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.” Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.

W. Ophunzirawo adati:

A. Ambuye, awa malupanga, tili nawo kale awiri.

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Chabwino. basi.

 

Kanyimbo

 

2. YESU ADAKAPEMPHERA KU MUNDA WA GETSEMANI.

W. Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazolowera. Ndipo ophunzira ake adapita naye. Pamene adafika kumeneko, Yesu adawauza kuti:

Y. Pempherani, kuti mungagwe m'zokuyesani.

W. Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera. Adati:

Y. Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautso chi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.

W. Pamenepo mngelo wochokera Kumwamba adamuwonekera namlimbitsa mtima. Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene linkadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi. Atapemphera, adaimirira napita kwa ophunzira ake. Adawapeza ali m'tulo chifukwa cha chisoni, ndipo adawafunsa kuti:

Y. Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.

W. Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankawatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone. Koma Yesu adamufunsa kuti:

Y. Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?

W. Ophunzira amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinali kuchitika, adafunsa Yesu kuti:

A. Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?

W. Apo m’modzi mwa iwo adatemadi wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Koma Yesu adati:

Y. Basi, lekani zimenezi.

W. Atatero adakhudza khutu la munthuyo namchiritsa. Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adawafunsa kuti:

Y. Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigawenga? Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m’Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthawi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.


Kanyimbo.


3. ANTHU AJA ADAPITA NDI YESU KU BWALO LA AYUDA.

 

W. Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankawatsatira chapatali. Iwo adasonkha moto m'kati mwa bwalo la nyumbayo, nakhala pansi pamodzi. Petro nayenso adakakhala pakati pao. Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati:

M. Awansotu anali naye.

W. Koma Petro adakana, adati:

M. Mai iwe, sindimdziwa ameneyu,

W. Patapita kanthawi pang'ono, munthu wina pomuwona adati:

M. Akulu inu, ndinunso mmodzi mwa iwo aja.

W. Koma Petro adati:

M. Munthu iwe, ai ndithu sindine.

W. Patapita ngati ora limodzi, munthu winanso adanenetsa kuti:

M. Ndithudi akulu awanso anali naye, pakuti ndi a ku Galileya.

W. Koma Petro adati:

M. Munthu iwe, sindikuzidziwa zimene ukunenazi.

W. Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira. Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, ‘lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.’ Pamenepo adatuluka, nakalira kwambiri chifukwa cha chisoni chachikulu. Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi

kumammenya. Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti:

A. Lota, wakumenya ndani?

W. Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe. Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita

naye ku Bwalo lao. Adamuuza kuti:

A. Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, utiwuze mosabisa.

W. Koma Iye adawayankha kuti:

Y. Ngakhale ntakuuzani, simungandikhulupirire konse, ndipo nditakufunsani funso, inu simungaliyankhe. Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthune ndidzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu Wamphamvuzonse.

W. Apo onse aja adati:

A. Tsono ndiye kutitu ndiwe Mwana wa Mulungu, ati?

W. Yesu adati:

Y. Mwanena nokha kuti ndine amene.

W. Pamenepo iwo aja adati:

A. Tikufuniranji umboni wina? Tadzimvera tokha mau akewa.

 

Kanyimbo


4. AKULU A AYUDA ADAPITA NAYE YESU KWA PILATO.

 

W. Gulu lonse lija lidanyamuka nkupita naye Yesu kwa Pilato. Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti:

A. Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.

W. Pilato adafunsa Yesu kuti:

M. Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?

W. Yesu adati:

Y. Mwanena nokha.

W. Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti:

M. Sindikumpeza mlandu munthuyu.

W. Koma iwo adaumirira nati:

A. Ameneyu amautsa mitima ya anthu ndi zimene amaphunzitsa m'dziko lonse la Yudeya. Adayambira ku Galileya, mpaka konse kuno.

W. Pamene Pilato adamva zimenezi, adawafunsa kuti:

M. Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?

W. Tsono atamva kuti ngwochokeradi ku dera limene Herode amalamulira, adamtumiza kwa Herodeyo, amene nayenso anali m' Yerusalemu masiku omwewo. Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthawi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china. Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri. Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato. Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana. Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba. Adawauza kuti:

M. Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokoneza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.

Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.

W: Pilatoyo ankayenera kuwamasulira mkaidi m’modzi pa nthawi ya chikondwerero cha Pasaka. Koma anthu onse aja adayamba kufuula pamodzi kuti:

A. Mchotseni ameneyu, mutimasulire Barabasi.

W. Barabasi anali atamponya m’ndende chifukwa cha kuyambitsa chipolowe mu mzinda, ndiponso kupha munthu. Pilato adafuna kumasula Yesu, motero adakakamba nawonso anthu aja. Koma iwo adafuulirafuulira kuti:

A. Mpachikeni! Mpachikeni!

W. Pilato adawafunsa kachitatu kuti:

M. Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.

W. Koma iwo adamuumiriza mokweza mau kuti Yesu apachikidwe. kufuula kwao kunkakulirakulira. Tsono Pilato adagamula kuti zimene anthu aja ankapempha zichitike. Adawamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m’ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna.


Kanyimbo.


5. ASIRIKALI ADAPITA NAYE KU GOLOGOTA KUTI AKAMPACHIKE PA MTANDA.

W. Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo. Anthu ambirimbiri ankamutsatira. Pakati pao panalinso akazi amene ankadzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumalira chifukwa cha Iye. Koma Yesu adawacheukira nawauza kuti:

Y. Inu azimai a ku Yerusalemu, musandilire Ine ai, koma mulire chifukwa cha inu nomwe ndi ana anu. Pakuti masiku akubwera pamene anthu azidzati, “ngodala azimai ouma, azimai osabala, azimai amene sadayamwitseko mwana.” Nthawi imeneyo adzapempha mapiri kuti, “tigwereni,” ndiponso magomo kuti, “tiphimbeni.” Pakuti ngati mtengo wauwisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?

W. Asilikali aja adaatenganso anthu ena awiri, amene anali zigawenga kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigawenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Yesu adati:

Y. Atate, muwakhululukire anthuwa, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.

W. Iwo aja adagawana zovala zake pakuchita maere. Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti:

A. Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.

W. Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. Adati:

A. Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.

W. Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m’Chigriki, m’Chilatini, ndi m’Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.” Chigawenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti:

M. Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.

W. Koma mnzake uja adamdzudzula, adati:

M. Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziwirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma awa sadachite cholakwa chilichonse.

W. Ndipo adati:

M. Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.

W. Yesu adamuyankha kuti:

Y. Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.

W. Nthawi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko, dzuwa litangoti bi kuda. Pamenepo chinsalu chotchinga chija cha m’Nyumba ya Mulungu chidang’ambika pakatimpakati. Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti:

Y. Atate ndikupereka mzimu wanga m’manja mwanu.

W. Atanena zimenezi, adatsirizika.


“Onse agwade ndikukhala chete kwa kanthawi.”

 

Kanyimbo


W. Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati:

M. Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.

W. Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni. Anthu onse amene ankadziwana ndi Yesu, ndiponso azimai amene adaamtsatira kuchokera ku Galileya, adaima patali nkumaona zimenezi. Panali munthu wina, dzina lake Yosefe, wa ku Arimatea, mudzi wina wa Ayuda. Anali munthu wabwino ndi wolungama, ndipo anali wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda. Komatu sankavomereza zimene anzake a m'Bungweli ankapangana, iye ankayembekeza kudza kwa Ufumu wa Mulungu. Iyeyu adapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Tsono adautsitsa naukulunga m’nsalu yoyera yabafuta, nkuuika m’manda. Mandawo anali asanaikemo munthu wina aliyense. Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene. Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m’mene adaaikira mtembo wa Yesu. Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose.

Mthenga wa Ambuye......Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, April 2, 2022

 


LAMULUNGU LA 05 MU LENTI - C
(Pita, usakachimwenso.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 43: 16 – 21 (Ndikuchita zinthu zatsopano ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa.)

Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiwatiwa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.”

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 126: 01 – 06.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,

Tinali ngati anthu amene akulota.

Pamenepo tidasekera kwambiri,

Ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti,

Chauta wawachitira zazikulu.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,

ndipo tasangalala.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,

tikhale ngati mtsinje yam'chipululu.

Anthu amene amafesa akulira,

Adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Munthu amene amapita akulira,

Atatenga mbeu zokafesa, adabwerera kwao

Akufuula ndi chimwemwe,

Atatenga mitolo yake yambiri.

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 03: 08 – 14 (Ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu.)

Abale, zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu, Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira. Chimene ndikufuna nchakuti ndidziwe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zowawa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi pokhulupirira kuti inenso ndidzakhala ndi moyo wosatha podzauka kwa akufa. Za kuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liwiro. Sindikunena kuti ndafikapo kale pa zimenezi, kapena kuti ndine wangwiro kale. Koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuzipata pakuti ndicho chinali cholinga cha Yesu Khristu pakundikopa kuti ndikhale wake. Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiwala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto ampikisano wa liwirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOWELE 02: 12 – 13.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 08: 01 – 11. (Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala.)

Yesu adapita ku Phiri la Olivi. M'mamawa adabweranso ku Nyumba ya Mulungu. Anthu onse adadza kwa lye, Iyeyo nkukhala pansi nayamba kuwaphunzitsa. Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. Paja M'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?’ Adaamufunsa funsoli kuti amuyese ndi kumpeza chifukwa. Koma Yesu adawerama, nayamba kulemba pansi ndi chala chake. Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaweramuka nawauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.” Atatero, adaweramanso namalemba pansi. Koma iwo atamva zimenezi, adayamba kuchokapo m’modzim’modzi, kuyambira akuluakulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pompaja. Kenaka Yesu adaweramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi m’modzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...