Saturday, April 9, 2022

 


LAMULUNGU LA KANJEDZA (CHIYAMBI CHA MLUNGU WOYERA) CYCLE C

MTHENGA WABWINO (KU M’DIPITI): MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 19: 28 – 40 (Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye)

Yesu adatsogolera ophunzira ake kupita ku Yerusalemu. Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira awiri, nawauza kuti, “pitani m’mudzi mukuwonawo. Mukakangolowamo mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukam’masule, nkubwera naye kuno. Wina akakakufunsani kuti, ‘mukum’masuliranji?’ Mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito.”’ Awiriwo adapita, nakapezadi monga momwe Yesu adaawauzira. Pamene ankamasula mwanawabuluyo, eni ake adawafunsa kuti, “mukum’masuliranji, mwanawabuluyu?” Iwo adati, “Ambuye ali naye ntchito.” Tsono adapita naye kwa Yesu, nayamba kuyala zovala zao pa buluyo, nakwezapo Yesu. Pamene Yesu ankapita, anthu adamchitira ulemu pakuyala zovala zao mu mseu. Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. Adati, “ndi yodala Mfumu imene ilikudza m’dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti. “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuwa aleke zimenezi.” Iye adati, “ndikutitu iwowa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi?”

Mthenga wa Ambuye................. Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

PAMBUYO PA M’DIPITI.


MAWU OYAMBA: MAWU A BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 50: 04 – 07. (Sindidawabisire nkhope ondinyoza. Ndikudziwa kuti Chauta sadzandichititsa manyazi.)

Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziwe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M’mawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira. Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidawanyoze kapena kuwapandukira. Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidawabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwawo sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziwa kuti sadzandichititsa manyazi.

Mawu a Ambuye…………...Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 22: 08 – 09, 17 – 18, 19 – 20, 23 – 24.

Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Onse ondiwona amandiseka,

Amandikwenzulira ndi kupukuta mitu two.

Amati, “unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse.

Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.”


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu.

Aboola manja anga ndi mapazi anga.

Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang’anitsitsa,

Akukondwera poona kuti ndikuvutika.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Agawana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere.

Koma Inu Chauta musakhale kutali.

Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu.

Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu.

Ndidzati, ‘Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye.

Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye,

inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.’


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?


MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 02: 06 – 11. (Ali munthu choncho adadzichepetsa, koma Mulungu adamkweza kopambana.)

Abale, Yesu Khristu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingama ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphawi wa kapolo, ndi kukhala munthu monga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza. Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 02: 08 – 09.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!

Ambuye, adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Nchifukwa chake chimene Mulungu adamkweza kopambana nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!


MTHENGA WABWINO: KUSAUKA KWA YESU KHRISTU AMBUYE ATHU MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 22: 14 –– 23:56

W. – Wowerenga.

Y. – Yesu.

M. – Munthu.

A. – Anthu ena.


1. YESU ADACHITA PHWANDO LA PASAKA NAPANGA UKARISTIA.

W. Nthawi itakwana, Yesu adakakhala podyera pamodzi ndi atumwi ake aja. Tsono adawauza kuti:

Y. Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Pasaka pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zowawa. Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Pasaka, mpaka Pasakayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.

W. Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu adati:

Y. Kwayani, imwani nonsenu. Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.

W. Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati:

Y. Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.

W. Atatha kudya, adawapatsanso chikho, nati:

Y. Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira. Koma ndithudi wondipereka kwa adani akudya nane pamodzi pompano. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.

W. Apo onse adayamba kumafunsana kuti:

A. Kodi ndani mwa ife angachite zotere?

W. Tsono ophunzira aja adayamba kutsutsana kuti:

A. Kodi mwa ife amati wamkulu ndani?

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amawaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira. Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira. Inu ndinu amene mwakhala ndi Ine pa masautso anga onse. Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu. Ndikadzalowa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukawalimbitse abale akowa.

W. Apo Petro adati:

M. Ambuye, ndili wokonzeka kupita nanu ku ndende, ngakhale kufa kumene.

W. Koma Yesu adamuyankha kuti:

Y. Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziwa.

W. Yesu adawafunsa kuti:

Y. Nthawi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasowapo kanthu?

W. Iwo adati:

A. Iyai.

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga. Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, “Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.” Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.

W. Ophunzirawo adati:

A. Ambuye, awa malupanga, tili nawo kale awiri.

W. Yesu adawauza kuti:

Y. Chabwino. basi.

 

Kanyimbo

 

2. YESU ADAKAPEMPHERA KU MUNDA WA GETSEMANI.

W. Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazolowera. Ndipo ophunzira ake adapita naye. Pamene adafika kumeneko, Yesu adawauza kuti:

Y. Pempherani, kuti mungagwe m'zokuyesani.

W. Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera. Adati:

Y. Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautso chi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.

W. Pamenepo mngelo wochokera Kumwamba adamuwonekera namlimbitsa mtima. Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene linkadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi. Atapemphera, adaimirira napita kwa ophunzira ake. Adawapeza ali m'tulo chifukwa cha chisoni, ndipo adawafunsa kuti:

Y. Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.

W. Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankawatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone. Koma Yesu adamufunsa kuti:

Y. Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?

W. Ophunzira amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinali kuchitika, adafunsa Yesu kuti:

A. Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?

W. Apo m’modzi mwa iwo adatemadi wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Koma Yesu adati:

Y. Basi, lekani zimenezi.

W. Atatero adakhudza khutu la munthuyo namchiritsa. Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adawafunsa kuti:

Y. Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigawenga? Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m’Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthawi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.


Kanyimbo.


3. ANTHU AJA ADAPITA NDI YESU KU BWALO LA AYUDA.

 

W. Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankawatsatira chapatali. Iwo adasonkha moto m'kati mwa bwalo la nyumbayo, nakhala pansi pamodzi. Petro nayenso adakakhala pakati pao. Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati:

M. Awansotu anali naye.

W. Koma Petro adakana, adati:

M. Mai iwe, sindimdziwa ameneyu,

W. Patapita kanthawi pang'ono, munthu wina pomuwona adati:

M. Akulu inu, ndinunso mmodzi mwa iwo aja.

W. Koma Petro adati:

M. Munthu iwe, ai ndithu sindine.

W. Patapita ngati ora limodzi, munthu winanso adanenetsa kuti:

M. Ndithudi akulu awanso anali naye, pakuti ndi a ku Galileya.

W. Koma Petro adati:

M. Munthu iwe, sindikuzidziwa zimene ukunenazi.

W. Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira. Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, ‘lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.’ Pamenepo adatuluka, nakalira kwambiri chifukwa cha chisoni chachikulu. Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi

kumammenya. Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti:

A. Lota, wakumenya ndani?

W. Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe. Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita

naye ku Bwalo lao. Adamuuza kuti:

A. Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, utiwuze mosabisa.

W. Koma Iye adawayankha kuti:

Y. Ngakhale ntakuuzani, simungandikhulupirire konse, ndipo nditakufunsani funso, inu simungaliyankhe. Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthune ndidzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu Wamphamvuzonse.

W. Apo onse aja adati:

A. Tsono ndiye kutitu ndiwe Mwana wa Mulungu, ati?

W. Yesu adati:

Y. Mwanena nokha kuti ndine amene.

W. Pamenepo iwo aja adati:

A. Tikufuniranji umboni wina? Tadzimvera tokha mau akewa.

 

Kanyimbo


4. AKULU A AYUDA ADAPITA NAYE YESU KWA PILATO.

 

W. Gulu lonse lija lidanyamuka nkupita naye Yesu kwa Pilato. Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti:

A. Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.

W. Pilato adafunsa Yesu kuti:

M. Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?

W. Yesu adati:

Y. Mwanena nokha.

W. Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti:

M. Sindikumpeza mlandu munthuyu.

W. Koma iwo adaumirira nati:

A. Ameneyu amautsa mitima ya anthu ndi zimene amaphunzitsa m'dziko lonse la Yudeya. Adayambira ku Galileya, mpaka konse kuno.

W. Pamene Pilato adamva zimenezi, adawafunsa kuti:

M. Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?

W. Tsono atamva kuti ngwochokeradi ku dera limene Herode amalamulira, adamtumiza kwa Herodeyo, amene nayenso anali m' Yerusalemu masiku omwewo. Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthawi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china. Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri. Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato. Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana. Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba. Adawauza kuti:

M. Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokoneza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.

Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.

W: Pilatoyo ankayenera kuwamasulira mkaidi m’modzi pa nthawi ya chikondwerero cha Pasaka. Koma anthu onse aja adayamba kufuula pamodzi kuti:

A. Mchotseni ameneyu, mutimasulire Barabasi.

W. Barabasi anali atamponya m’ndende chifukwa cha kuyambitsa chipolowe mu mzinda, ndiponso kupha munthu. Pilato adafuna kumasula Yesu, motero adakakamba nawonso anthu aja. Koma iwo adafuulirafuulira kuti:

A. Mpachikeni! Mpachikeni!

W. Pilato adawafunsa kachitatu kuti:

M. Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.

W. Koma iwo adamuumiriza mokweza mau kuti Yesu apachikidwe. kufuula kwao kunkakulirakulira. Tsono Pilato adagamula kuti zimene anthu aja ankapempha zichitike. Adawamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m’ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna.


Kanyimbo.


5. ASIRIKALI ADAPITA NAYE KU GOLOGOTA KUTI AKAMPACHIKE PA MTANDA.

W. Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo. Anthu ambirimbiri ankamutsatira. Pakati pao panalinso akazi amene ankadzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumalira chifukwa cha Iye. Koma Yesu adawacheukira nawauza kuti:

Y. Inu azimai a ku Yerusalemu, musandilire Ine ai, koma mulire chifukwa cha inu nomwe ndi ana anu. Pakuti masiku akubwera pamene anthu azidzati, “ngodala azimai ouma, azimai osabala, azimai amene sadayamwitseko mwana.” Nthawi imeneyo adzapempha mapiri kuti, “tigwereni,” ndiponso magomo kuti, “tiphimbeni.” Pakuti ngati mtengo wauwisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?

W. Asilikali aja adaatenganso anthu ena awiri, amene anali zigawenga kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigawenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Yesu adati:

Y. Atate, muwakhululukire anthuwa, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.

W. Iwo aja adagawana zovala zake pakuchita maere. Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti:

A. Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.

W. Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. Adati:

A. Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.

W. Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m’Chigriki, m’Chilatini, ndi m’Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.” Chigawenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti:

M. Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.

W. Koma mnzake uja adamdzudzula, adati:

M. Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziwirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma awa sadachite cholakwa chilichonse.

W. Ndipo adati:

M. Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.

W. Yesu adamuyankha kuti:

Y. Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.

W. Nthawi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko, dzuwa litangoti bi kuda. Pamenepo chinsalu chotchinga chija cha m’Nyumba ya Mulungu chidang’ambika pakatimpakati. Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti:

Y. Atate ndikupereka mzimu wanga m’manja mwanu.

W. Atanena zimenezi, adatsirizika.


“Onse agwade ndikukhala chete kwa kanthawi.”

 

Kanyimbo


W. Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati:

M. Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.

W. Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni. Anthu onse amene ankadziwana ndi Yesu, ndiponso azimai amene adaamtsatira kuchokera ku Galileya, adaima patali nkumaona zimenezi. Panali munthu wina, dzina lake Yosefe, wa ku Arimatea, mudzi wina wa Ayuda. Anali munthu wabwino ndi wolungama, ndipo anali wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda. Komatu sankavomereza zimene anzake a m'Bungweli ankapangana, iye ankayembekeza kudza kwa Ufumu wa Mulungu. Iyeyu adapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Tsono adautsitsa naukulunga m’nsalu yoyera yabafuta, nkuuika m’manda. Mandawo anali asanaikemo munthu wina aliyense. Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene. Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m’mene adaaikira mtembo wa Yesu. Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose.

Mthenga wa Ambuye......Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...