LAMULUNGU LA 04 PA CHAKA C
(Yesu adabwera kwawo, koma anthu ake adampeputsa.)
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 01: 04 – 05, 17 – 19. (Ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.)
Chauta adandiuza kuti, “ndisanakulenge m’mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziwa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse. Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukawauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuona. Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuwa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m’dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa.”
Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-----------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 71: 01 – 06, 15, 17.
Pakamwa panga padzalankhula za
chipulumutso chanu.
Ine ndimathawira kwa Inu Chauta,
Musandichititse manyazi,
Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa,
Pakuti ndinu Mulungu wolungama,
Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo
mundipulumutse.
Pakamwa panga padzalankhula za
chipulumutso chanu.
Mundikhalire thanthwe lothawirako,
Ndiponso linga lolimba lopulumukirako,
Inu ndinu thanthwe langa ndi linga
langa,
Landitseni Inu Mulungu wanga kwa
anthu oipa.
Pakamwa panga padzalankhula za
chipulumutso chanu.
Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani,
Inu Chauta, ndinu amene
ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga,
Inu mwakhala wondichirika kuyambira
pa nthawi imene ndidabadwa,
Inu ndinu amene mudanditulutsa m’mimba
mwa mai wanga.
Pakamwa panga padzalankhula za
chipulumutso chanu.
Pakamwa panga padzalankhula tsiku
lililonse,
Za ntchito zanu zolungama ndi za
chipulumutso chanu,
Inu Mulungu, mwandiphunzitsa
kuyambira ubwana wanga,
Ndipo ndikulalikabe ntchito zanu
zodabwitsa.
Pakamwa panga padzalankhula za
chipulumutso chanu.
------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12: 31 – 13:13. (Zilipo zinthu zitatuzi, chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwazonsezi chopambana ndi chikondi.)
Abale, inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni. Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziwa zobisika zonse, ndikumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiliro chachikulu chakuti ndingathe kusintha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale nditagawira amphawi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe. Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndiponso sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangawa. Sichikondwera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthawi, sichitaya mtima, ndipo chimapirira nthawi zonse. Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziwika kudzaleka, ndipo nzeru za anthu zidzatha. Paja timangodziwa zinthu moperewera, ndipo kulalika kwathunso nkoperewera, koma changwiro chikadzaoneka, chopereweracho chidzatha. Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo. Tsopano timaona zinthu ngati m’galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthawiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziwa moperewa, koma pa nthawiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziwira ine kotheratu. Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Mawu
a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-----------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: LUKA 04: 18.
Alleluia, Alleluia – Ambuye wandidzoza
kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende
kuti adzamasulidwa – Alleluia, Alleluia.
-------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 04: 21 – 30. (Monga adachitira Eliya ndi Elisha, Yesu Khristu sanatumizidwe kwa Ayuda okha.)
Anthu onse adamtamanda Yesu, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “kodi uyu si mwana wa Yosefeyu?” Apo Yesu adawauza kuti, “ndithudi mudzandiuza mwambi uja wakuti, iwe sing’anga, dzichiritse wekha. Mudzatinso, tidamva zimene mudachita ku Karpenao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.” Adawauzanso kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao. Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthawi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m’dziko lonse. Eliya sadatumidwe ndi kwa mmodzi yemwetu mwa iwo aja, koma adatumidwa kwa mai wamasiye wa ku mudzi wa Sarepta, mdziko la Sidoni. Panalinso akhathe ambiri pakati pa Aisraele nthawi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.” Anthu onse amene anali m’nyumba yamapemphero muja atamva mau amenewa, adapsa mtima kwambiri. Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi, koma Iye adangodutsa pakati pao, nkumapita.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog:
No comments:
Post a Comment