LAMULUNGU LA 05 PA CHAKA C
(Ambuye! Ndilipo, munditume.)
Chaka chimene mfumu Uziya
adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa.
Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse.
Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi:
awiri ophimbira kumaso, awiri ophimbira mapazi, awiri oulukira. Aserafiwo
ankafuulirana kuti, “ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse,
ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi. Chifukwa cha kufuulako maziko onse
ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m’Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha. Apo ine
ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa,
ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu,
Chauta Wamphamvuzonse.” Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja adaulukira kwa ine, ali
ndi khala lamoto m’manja mwake. Khalalo adalichotsa pa guwa la nsembe ndi
mbaniro. Ndipo adandikhuza pakamwa ndi khala lamotolo nati, “taona, ndakukhudza
milomo ndi khalali. Kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?”
Apo ndidati, “ndilipo ineyo, tumeni.”
Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-----------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138: 01 – 05, 07 –
08.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi
mtima wanga wonse,
Ndikuimba nyimbo zokutamandani
pamaso pa milungu,
Ndikugwada mowerama,
Kunyumba kwa Nyumba yanu yoyera.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Ndikutamanda dzina lanu,
Chifukwa cha chikondi chanu
chosasinthika,
Chifukwanso cha kukhulupirika kwanu,
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu
mudandiyankha,
Mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu
zanu.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Mafumu onse a m’dziko
adzakutamandani, Inu Chauta,
Chifukwa amva mau a pakamwa panu,
Adzaimba nyimbo zotamanda njira za
Chauta,
Pakuti ulemerero wa Chauta ndi
waukulu.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Mumatambasula dzanja lanu kuletsa
adani anga okwiya,
Dzanja lanu lamanja
limandipulumutsa,
Chikondi chanu, Inu Chauta,
nchamuyaya,
Muipitirize ntchito imene
mwaiyambayo.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
------------------------------
MAWU
ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO:
1 AKORINTO 15: 01 – 11. (Zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira
ndi zomwezonso.)
Abale,
ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira,
ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba. Mulungu adzakupulumutsani
ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani.
Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe. Pajatu mau aakulu amene
ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu
adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Adaikidwa m'manda, mkucha wake
adauka, monga Malembo anenera. Motero adaonekera Kefa, kenaka atumwi khumi ndi
awiri aja. Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthawi
imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira. Ndipo adaonekera Yakobo,
kenaka atumwi onse. Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo,
ngakhale ndili ngati mpolo chabe. Inetu ndine wamng'onong'onodi mwa atumwi
onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza
Mpingo wa Mulungu. Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili
monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza
kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira,
koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa. Motero kaya ndi ineyo kaya
ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi
zomwezonso.
Mawu
a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-----------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: MATEYO
04: 19.
Alleluia, Alleluia – Inu,
munditsate, atero Ambuye, ndikakusandetseni asodzi a anthu – Alleluia,
Alleluia.
-------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA
WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 05: 01 – 11. (Adasiya zonse namatsata Yesu.)
Tsiku lina
Yesu adamirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete, anthu ambirimbiri
nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu. Iye adaona zombo ziwiri pamphepetepo.
Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao. Yesu adalowa m'chombo
chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku
nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuwaphunzitsa
anthuwo. Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, "Sunthirani kozamako,
muponye makoka anu kuti muphe nsomba." Simoni adati, "Aphunzitsi,
usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo
mwatero, chabwino ndiponya makoka." Tsono iwo adaponyadi makoka, napha
nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika. Adachita
kukodola anzao a m'chombo china chija kuti adzawathandize. Iwo adabwera, ndipo
adadzaza zombo ziwiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira. Pamene Simoni
Petro adaona zimenezo, adagwada nkuwerama kwambiri pamaso pa Yesu nati,
"Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa." Adaatero popeza
kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa
nsomba zimene adaaphazo. Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni,
nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, "Usaope, kuyambira
tsopano udzakhala msodzi wa anthu." Motero, atakokera zombozo ku mtunda,
adasiya zonse namatsata Yesu.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog:
No comments:
Post a Comment