Saturday, January 29, 2022


 LAMULUNGU LA 04 PA CHAKA C

(Yesu adabwera kwawo, koma anthu ake adampeputsa.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 01: 04 – 05, 17 – 19. (Ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.)

Chauta adandiuza kuti, “ndisanakulenge m’mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziwa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse. Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukawauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuona. Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuwa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m’dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa.”

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 71: 01 – 06, 15, 17.

Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu.

 

Ine ndimathawira kwa Inu Chauta,

Musandichititse manyazi,

Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa,

Pakuti ndinu Mulungu wolungama,

Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse.

 

Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu.

 

Mundikhalire thanthwe lothawirako,

Ndiponso linga lolimba lopulumukirako,

Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

Landitseni Inu Mulungu wanga kwa anthu oipa.

 

Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu.

 

Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani,

Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga,

Inu mwakhala wondichirika kuyambira pa nthawi imene ndidabadwa,

Inu ndinu amene mudanditulutsa m’mimba mwa mai wanga.

 

Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu.

 

Pakamwa panga padzalankhula tsiku lililonse,

Za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu,

Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga,

Ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa.

 

Pakamwa panga padzalankhula za chipulumutso chanu.

------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12: 31 – 13:13. (Zilipo zinthu zitatuzi, chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwazonsezi chopambana ndi chikondi.)

Abale, inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni. Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziwa zobisika zonse, ndikumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiliro chachikulu chakuti ndingathe kusintha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale nditagawira amphawi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe. Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndiponso sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangawa. Sichikondwera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthawi, sichitaya mtima, ndipo chimapirira nthawi zonse. Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziwika kudzaleka, ndipo nzeru za anthu zidzatha. Paja timangodziwa zinthu moperewera, ndipo kulalika kwathunso nkoperewera, koma changwiro chikadzaoneka, chopereweracho chidzatha. Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo. Tsopano timaona zinthu ngati m’galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthawiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziwa moperewa, koma pa nthawiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziwira ine kotheratu. Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: LUKA 04: 18.

Alleluia, Alleluia – Ambuye wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa – Alleluia, Alleluia.

-------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 04: 21 – 30. (Monga adachitira Eliya ndi Elisha, Yesu Khristu sanatumizidwe kwa Ayuda okha.)

Anthu onse adamtamanda Yesu, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “kodi uyu si mwana wa Yosefeyu?” Apo Yesu adawauza kuti, “ndithudi mudzandiuza mwambi uja wakuti, iwe sing’anga, dzichiritse wekha. Mudzatinso, tidamva zimene mudachita ku Karpenao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.” Adawauzanso kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao. Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthawi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m’dziko lonse. Eliya sadatumidwe ndi kwa mmodzi yemwetu mwa iwo aja, koma adatumidwa kwa mai wamasiye wa ku mudzi wa Sarepta, mdziko la Sidoni. Panalinso akhathe ambiri pakati pa Aisraele nthawi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.” Anthu onse amene anali m’nyumba yamapemphero muja atamva mau amenewa, adapsa mtima kwambiri. Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi, koma Iye adangodutsa pakati pao, nkumapita.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: Mkatolikamw

Saturday, January 22, 2022

LAMULUNGU LA 03 PA CHAKA C


LAMULUNGU LA 03 PA CHAKA C (Mau anu ndi opatsa moyo wosatha.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NEHEMIYA: NEHEMIYA 08: 02 – 06, 08 – 10. (Ezara adawerenga buku la Malamulo, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino.)

Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Tsono Ezara adawerenga bukulo atayang’ana bwalo la chipata cha madzi, kuyambira m’mamawa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zowerengazo. Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Kudzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu. Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira. Kenaka Ezara adati, “atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaweramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire. Aleviwo adawerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino. Tsono bwanamkubwa Nehemiya, pamodzi ndi Ezara wansembe ndi Mphunzitsi wa malamulo, kudzanso Alevi amene ankaphunzitsa anthu, adauza anthu onse aja kuti, “lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Ndiye kuti anthu onse ankalira atamva mau a Malamulowo. Tsono Nehemiya adapititriza nati, “kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muwapetseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19: 08 – 10, 15.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Mau a Chauta ngangwiro,

Amapatsa munthu moyo watsopano,

Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika,

Umawapatsa nzeru amene alibe.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Malangizo a Chauta ndi olungama,

Amasangalatsa mtima,

Malamulo a Chauta ndi olungama,

Amapatsa mtima womvetsa.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

Chimakhala mpaka muyaya,

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

Ncholungama nthawi zonse.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Mau anga ndi maganizo anga,

Avomerezeke pamaso panu,

Inu Chauta, thanthwe langa,

Ndi Mpulumutsi wanga.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

----------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12: 12 – 21, 27. (Inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.)

Abale, Khristu ali ngati thupi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri. Nanga phazi litanena kuti, “poti sindine dzanja, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Nanga khutu litanena kuti, “poti sindine diso, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Kodi thupi lonse likadakhala diso lokha, bwenzi munthu akumva bwanji? Kapena thupi lonse likadakhala khutu lokha, bwenzi munthu akuninkhiza bwanji? Koma m’mene ziliri Mulungu adaika chiwalo chilichonse pamalo pake m’thupi, monga momwe adafunira. Ziwalo zonse zikadangokhala chiwalo chimodzi, sipakadakhala thupi konse. Komatu ziwalo nzambiri, ngakhale thupi ndi limodzi lokha. Motero diso silingauze dzanja kuti, “ndilibe nawe ntchito.” Ndiponso mutu sungauze mapazi kuti, “ndilibe nanu ntchito.” Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: LUKA 04: 18.

Alleluia, Alleluia – Ambuye wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa. – Alleluia, Alleluia.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 01: 01 – 04; 04: 14 – 21. (Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwawamva.)

Ateofilo olemekezeka, anthu ambiri adayesa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu. Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziwona chamaso kuyambira pachiyambi pake, nakhala akuzilalika. Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m’mene zonsezo zidaachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane. Ndatero kuti mudziwe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi. Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonseli. Ankaphunzitsa m’nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda. Nthawi ina Yesu adafika ku Nazerete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adalowa m’nyumba yamapemphero, monga adazolowera, naimirira kuti awerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikawapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthawi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m’nyumbamo ankangomupenyetsetsa. Tsono Yesu adawauza kuti, “lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvawa.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Mkatolikamw

 

 

Saturday, January 15, 2022

LAMULUNGU LA 02 PA CHAKA C


 LAMULUNGU LA 02 PA CHAKA C

(Ophunzira ake adamkhulupirira)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 62: 01 – 05. (Mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi.)

Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala, ndipo chipulumutso chake chitaoneka ngati muuni woyaka. Iwe Yerusalemu, mitundu ya anthu idzakuwona utapambana pa nkhondo, mafumu ao onse adzaona ulemerero wako. Adzakuitanira dzina latsopano, limene adzakutcha ndi Chauta yemwe. Udzakhala ngati chisoti chaufumu chokongola m’manja mwa Chauta, ngati msangamutu yaulemerero m’manja mwa Mulungu wako. Sudzatchedwanso ‘wosiyidwa’, dziko lako silidzatchedwanso ‘chipululu’. Dzina lako latsopanolo lidzakhala ‘ndikukondwera naye’. Dziko lako lidzatchedwa ‘wokwatiwa mwachimwemwe’, chifukwa choti Chauta akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako. Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01 – 03, 07 – 10.

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!

Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

Lengezani za ulemerero wake,

Kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa,

Kwa anthu a m’maiko onse.

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

Tamandani, inu anthu a mitundu yonse,

Vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake,

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera,

Njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi,

Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu.”

Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12: 04 – 11. (Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amagawira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgawira.)

Abale, pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kulankhula mau olangiza anthu. Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda. Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziwika, ndipo amapatsa wina mphatso za kutanthauzira zilankhulozo. Amene amachititsa anthu zonsezi ndi Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Amagawira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgawira.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: 2 ATESALONIKA 02: 14.

Alleluia, Alleluia – Mulungu adakuitanani kudzera mwa Uthenga Wabwino kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. – Alleluia, Alleluia.

-------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 02: 01 – 11. (Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m’mudzi wa Kana m’dera la Galileya.)

Kunali Ukwati ku mudzi wa Kana m’dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko. Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “wawathera vinyo.” Yesu adayankha kuti, “Mai kodi mukuti nditani? Nthawi yangatu siinafike.” Apo mai ake adauza anyamata amene ankatumukira kuti, “chilichonse chimene akuuzeni, muchite.” Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M’mbiya iliyonse munkalowa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo. Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “dzadzani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzadza mpaka m’milomo. Pambuyo pake adawauza kuti, “tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa mphwando.” Iwowo adakaperekadi. Mkulu wa phwandoyo adalawa madzi osanduka vinyoyo osadziwa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziwa.) Tsono mkulu wa mphwandoyo adaitana mkwati, namuuza kuti, “anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amawapatsa vinyo wokoma pang’ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.” Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m’mudzi wa Kana m’dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: Mkatolikamw

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...