Saturday, June 21, 2025

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

“Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (CHIYAMBI); GENESIS 14:18-20. (Adatenga buledi ndi vinyo).

 

Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga Buledi ndi Vinyo. Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu. Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zimene adaalandira.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 110:1-4.

 

Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja,

mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”

 

Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Chauta adzakuza ufumu wako wamphamvu kuchokera ku Ziyoni.

Adzati, “Khala mfumu yolamulira adani ako.”

 

Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Anthu ako adzadzipereka mwaufulu pa tsiku limene udzaonetse mphamvu zako pa phiri loyera.

Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu unyinji wao, monga m’mene mame amabwerera m’mamawa.

 

Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Chauta walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake akuti,

“Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”

 

Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 1 AKORINTO 11:23-26. (Nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye).

 

Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.’’ Momwenso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthawi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.’’ Pakuti nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—Yohane 6:51.

Alleluia, Alleluia!! – Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

NYIMBO YA UKARISTIA (SEQUENCE)

 

O SIYONI UYAMIKE

Mbusa wabwino, Buledi weniweni,

Mbuye Yesu, mutichitire chisoni.

Muteteze, nkulowetsa

Nkhosa zanufe kumwamba.

 

1. O Siyoni, uyamike

Mpulumutsi wako, Mbuye,

Mfumu ndinso Mbusa wako.

 

2. Sudzafika kuimbira

Mlungu wako mokwanira.

Ukwezetu mawu ako.

 

3. Nkofunika ndithu lero

Kutama Buledi wamoyo,

Ngwopatsa moyo womwewo.

 

4.Tidziwa mosapeneka

Kuti Yesu anapatsa

Bulediyu kwa apositoli.

 

5. Tsono tisankhule nyimbo

Zokoma kwambiri lero

Ndi kuimba mwachimwemwe.

 

6. Misa itibweretsera

Tsiku lomwe la kupanga

Phwando loyerayerali.

 

7. Ndi Pasaka yatsopano

Ya Mfumu yatsopanonso

Miyambo yakale yatha.

 

8. Zalero zibadiritsa

Zakale, monga kuyera

M'mawa kuchotsatu mdima.

 

9. Yesu anatilamula

Kubwereza zomwe zija

Anazichita tsikuli.

 

10. Pomvera Yesu ifenso

Tisandutsa buledi n'vinyo

Pa nsembe yopulumutsa.

 

11. Buledi asanduka Thupi

Ndiponso vinyo Magazi

A Khristu, Ambuye athu.

 

12. Sitimvetsa, sitiona,

Koma ndithu tizimvera

Zozizwitsa zimenezi.

 

13. Buledi ndinso vinyo ali

Chizindikiro chophimba

Zazikulu zobisika.

 

14. Tidya Thupi la Ambuye

Ndi kumwa Magazi ake:

Akhala muziwirizi.

 

15. Aliyense amlandira

Wathunthudi, wosasweka,

Ndi wosagawika konse.

 

16. Nayo Buledi wa anjelo

Ngwa alendofe tsopano

Manna wotipatsa nyonga.

 

17. Mulungu wamphamvuzonse

Ndiponso wodziwa zonse,

Inu mutidyetsa pano.

 

18. Mutidyetsenso Kumwamba

M'phwando la anthu oyera.

Amen. Amen. Aleluya.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 9:11b-17. (Anthu onse aja adadya nakhuta).

 

Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adawalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuwa lili pafupi kulowa, ophunzira khumi ndi awiri aja adadzauza Yesu kuti, “bwanji anthuwa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.’’ Koma Yesu adawauza kuti, “inuyo apatseni chakudya.’’ Iwo adati, “tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziwiri zokha. Kaya kapena tipite tikawagulire anthu onsewa chakudya?’’ Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “auzeni anthuwa akhale pansi m’magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.’’ Ophunzira aja adawakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziwiri zija, nayang’ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi awiri.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti nsembe ya Ukaristia ndi gwero la zabwino za chipulumutso, tigwirizane naye Yesu Khristu wansembe wathu wamuyaya, popereka mapemphero athu kwa Mulungu Atate:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti apeze m’sakramenti la Ukaristia mphamvu zoyeretsa moyo wao wa tsiku ndi tsiku, pakuphathana kwenikweni ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere anthu onse amene akusauka ndi njala, matenda ndi umphawi, kuti apeze chithandizo chochokera kwa anzawo achikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anyamata amene Mulungu akuwaitana ku unsembe kuti avomere kuitanidwa kwao ndipo alimbikire pa maphunziro ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tipemphererane ife tonse a m’parishi yathu ino, kuti tikhale amodzi ndi kumakondana mwaubale, pakulandira Ukaristia kawirikawiri.
Tikupemphani, mutivomereze.


Atate, tikukuyamikani, chifukwa potiitana ku phwando loyerali, mwatipatsa mwai wa kulumikizana tonse m’chikondi chanu. Mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, June 14, 2025

Chaka cha Utatu Woyera—C

Chaka cha Utatu Woyera—C

“Tiyamike Mulungu Atate ndi Mwana ndinso Mzimu Woyera.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA MIYAMBO: MIYAMBO 8:22-31. (Lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, Ine ndinalipo kale).

 

Nzeru ya Mulungu imafuula kuti: “Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambilira ndinali ine. Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe. Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale. Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo; lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi. Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire anyanja yozama, pamene ankaika thambo m’malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m’nyanja yozama, pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi. Nthawiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthawi zonse. Ndinkasangalala m’dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 8:4-5, 6-7, 8-9.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Ndikamayang’ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu,

Ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti,

“Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Ndiyetu mudamlenga mochepera pang’ono kwa Mulungu amene,

Mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu,

Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu,

Mudamgonjetsera zolengedwa zonse.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Nkhosa, ng’ombe ndi nyama zakuthengo,

Mbalame zamumlengalenga, nsomba za m’nyanja,

Ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 5:1-5. (Tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu).

 

Abale, popeza kuti pakukhulupilira tapeza kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa Mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupilira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandilako ulemelero wa Mulungu. Koma sipokhapo ai, timakondweranso m’masautso athu. Pakuti tikudziwa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa la moto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—
Chibvumbulutso 1:8.

 

Alleluia, Alleluia!! – Ulemu ukhale kwa Atate ndi Mwana ndi Mzimu Woyera, Mulungu amene alipo, amene analipo, amene alikudza. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 16:12-15. (Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzakutenga zochokera kwa Ine, nadzakudziwitsani inu).

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuwamvetsa tsopano ayi. Koma akadzafika Mzimu wodziwitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ayi, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziwitsani zinthu zam’tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziwitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa ine, nadzakudziwitsani inu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tidalandira Mzimu Woyera wotitsimikizira kuti ndife ana a Mulungu ndithu. Tiyeni, tipemphe Atate athu a Kumwamba, mogwirizana ndi Mwana wao Yesu, kuti adalitse anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti kukondana kwao kutsimikize kuti iwo adasandukadi ana a Mulungu ndi abale ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere onse osadziwa Mthenga Wabwino kuti Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwafikitsa ku chikhulupiriro cha chikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja onse kuti eniake akhale okondana ndipo apereke chitsanzo chabwino kwa ana awo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tipemphererane kuti timange moyo pa chikondi cha Mulungu pomaonetsa anthu onse mtima wachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

 

Mulungu Atate athu, tikukuthokozani chifukwa mwatiwonetsa nkhope yanu ndiponso kukoma mtima kwanu mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, June 7, 2025

Chaka cha Kutsika kwa Mzimu Woyera kwa Apositoli (Pentecost Sunday)—C

 

Chaka cha Kutsika kwa Mzimu Woyera kwa Apositoli (Pentecost Sunday)—C

“Adawauzira mpweya wopatsa moyo.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 2:1-11. (Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula).

 

Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m’nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalawi ta moto tooneka ngati malilime tikugawikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankawalankhulitsira. Tsono, m’Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankawamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “kodi onse akulankhulawa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuwamva akulankhula chilankhulo chakwawo? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesapotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, Ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuwamva anthuwa akulankhula m’zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 104:1, 24, 29-31.

 

Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri,

Inu Chauta ntchito zanu zambiri,

Ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu

 

Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.

 

Mukazichotsera mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi,

Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa,

Ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.

 

Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.

 

Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,

Chauta akondwe nazo ntchito zakezo,

Mapemphero anga amkomere Chauta,

Popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.

 

Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 8: 8-17. (Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu).

 

Abale, anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m’moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, ‘Abba! Atate!’ Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nso madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------


[KAPENA]


MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA:
 MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORITO; 1 AKORINTO 12: 3b-7, 12-13 (Tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi).

 

Abale, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, ‘Yesu ndi Ambuye.’

Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera m’modzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi m’modzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakuti yakuti yoti ayigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


N
YIMBO YA PENTEKOSTE (SEQUENCE) [Nyimboyi itha kunenedwa kapena kuyimbidwa]

 

1.     Bwerani Mzimu Woyera,

Tumizani kuwala kwanu,

Kufumira kumwambako.

 

2.     Bwerani, Tate wa amphawi,

Bwerani, wopatsa mphatso,

Inu muuni wa mitima.

 

3.     Ndinu Msangalatsi ndithu,

Woyendera mitima yathu,

Kuti mudzaithuzitsa.

 

4.     Pa ntchito ndinu Mpumulo,

Mumatichotsera kutentha,

Ndi kutsangula misozi yathu.

 

5.     Ndinu kuwala kokoma,

Dzazani mitima yathu,

Ya ife anthu okumverani.

 

6.     Mutapanda kudzamthandiza,

Munthu sangapeze kanthu,

Zonse zidzamuipira.

 

7.     Tsukani zoipa zathu,

Dzatsirireni zouma,

Chiritsani mabala athu.

 

8.     Dzafewetseni zolimba,

Funditsani zozizira,

Lungamitsani zokhota.

 

9.     Tipatseni anthu anufe,

Okhulupirira Inu,

Mphatso zisanu ndi ziwiri.

 

10.  Kometsani makhalidwe athu,

Katifikitseni kumwamba,

Kukadala nthawi zonse,

Amen.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

 

Alleluia, Alleluia!! – Bwerani Mzimu Woyera, mudzaze m’mitima ya anthu okhulupirira ndipo chikondi chanu chikhazikike mwa iwo. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 14: 15-16, 23-26. (Mzimu Woyera ndiye adzakuphunzitseni zonse).

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa ife. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvawa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------


[KAPENA]

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 19-23 (Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani. Landirani Mzimu Woyera).

 

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’thiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira m’pweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Mzimu Woyera amene wakhazikika mwa ife akutitsimikizira kuti ndifedi ana a Mulungu. Tiyeni tsono, timupemphe kuti apitirize ntchito zake zamphamvu mwa ife ndi mwa anthu onse:

1.     Tipempherere akulu oyang’anira Mpingo wa Mulungu, kuti asenze udindo wao molimbika ndi mwachikondi, potsata mphamvu zochokera kwa Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu onse, kuti Mzimu Woyera alunzitse mitima yao ndi kuwakhazikitsa m'chikondi chake, kuti akhale Mpingo umodzi ndithu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anthu onse amene akadali mu mdima, osadziwa Mthenga Wabwino, kuti Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwalondoloza m’njira ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tipemphererane ife tonse amene tasonkhana lero, kuti tigwiritse ntchito nzeru ndi mphamvu zofumira kwa Mzimu Woyera, pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.
Tikupemphani, mutivomereze.


Atate okoma mtima, mudakwaniritsa malonjezo anu pakutitumizira Mzimu Woyera. Mudzaze mitima ya anthu onse ndi mphatso zake zamphamvu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...