CHAKA CHA UBATIZO WA AMBUYE YESU – C.
“Iye ndiye Mwana wanga wapamtima.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 42:1-4,6-7. (Nayu Mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye).
Chauta akuti, “nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankha, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo. Sadzafuula kapena kukweza mau, mau ake sadzamveka mu mseu. Bango lopindika sadzalithyola, moto wozilala sadzauzima. Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika. Sadzafookera kapena kutaya mtima, mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi. Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake. “Ine Chauta ndakuitana kuti ukhazikitse chilungamo. Ndakugwira padzanja ndi kukusunga. Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu, ukhale kuwala kounikira anthu a mitundu ina. Udzawatsekula maso athu akhungu, udzamasula akaidi m’ndende, udzatulutsa m’ndende anthu okhala mu mdima.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 29:1-4,9-10.
Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere
Tamandani Chauta, inu okhala kumwamba,
Tamandani ulemerero wake ndi mphamvu zake,
Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta,
Mumpembedze mu Ulemu wa ungwiro wake.
Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere
Liwu la Chauta likumveka pamwamba pa nyanja,
Liwu lake lamveka pa nyanja yaikulu,
Liwu la Chauta ndi lamphamvu,
Liwu la Chauta ndi laulamuliro.
Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere
Liwu la Chauta likuzunguza miwanga,
Onse a m’nyumba mwake akufuula kuti, “Ulemererewo!”
Chauta amalamulira nyanja zonse,
Amakhala kwamuyaya pa mpando wake wachifumu.
Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 10:34-38. (Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu).
Petro adayamba kulankhula, adati, “zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo. Mukudziwa kuti adatumizira Aisraele mau ake nawauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 9:7.
Alleluia, Alleluia – Padafika mtambo ndipo mu mtambomo mudamveka mau a Atate akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.” – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 3:15-16,21-22. (Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka).
Pa nthawi yomweyo, chiyembekezo cha anthu chidayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane kuti kapena ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Tsono Yohane Ankawauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m’moto.” Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mzimu Woyera wokhala mwa ife akutitsimikizira kuti ndifedi ana a Mulungu; tiyeni tsono tipemphe Atate athu a Kumwamba madalitso ao.
1. Atsogoleri a Mpingo asenze udindo wao molimbika, podziwa kuti alikupitiriza ntchito ya Yesu Khristu pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko, Mzimu Woyera angolere nzeru zao, adziwe kulondoloza anthu a m'njira ya chilungamo ndi mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, akhale ndi mtima wosirira kusanduka nawonso ana a Mulungu ndi atumiki ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tasonkhana muno, Atate atidzaze ndi Mzimu wake wachikondi, nafenso tizichita ntchito zabwino ponseponse potsanzira Yesu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, potula mapemphero athuwa m’manja mwanu, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa mudatisandutsa ana anu ndi atumiki anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment