“Yesu Mpulumutsi adadzera anthu a mitundu yonse.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 60:1-6. (Ulemerero wa Chauta udzawoneka).
Iwe Yerusalemu dzuka, wala, kuwala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuwalira. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuwalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Anthu a mitundu ina adzatsata kuwala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuwa limene likutuluka kumene. Yang’ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m’manja ngati ana. Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe. Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing’onozing’ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72:1-2,7-8,10-13.
Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.
Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,
Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,
Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,
Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.
Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.
Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo,
Mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso,
Mafumu onse adzaigwadira,
Ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.
Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,
Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,
Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,
Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.
Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 3:2-3,5-6. (Chinsinsicho nchakuti anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda).
Abale, kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake. Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa. Chinsinsi chimenecho anthu a mibadwo yakale sadachidziwe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake. Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 2:2.
Alleluia, Alleluia – Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 2:1-12. (Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye).
Yesu adabadwira m’mudzi wa Betelehemu, m’dziko la Yudeya, pa nthawi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “ali kuti mwana amene adabadwa kuti akhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu onse a m’Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Tsono Herode yo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, nawafunsa kuti, “kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” Iwo adati, “M’mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti, Iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe wamng’ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri amene adzalamulira anthu anga Aisraele.” Pamenepo Herode adawaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, nawafunsitsa za nthawi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. Kenaka adawatumiza ku Betelehemu nkuwauza kuti, “pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziwitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idawatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adalowa m’nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adawachenjeza m’maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tonse taitanidwa kudzalandira chipulumutso mwa Yesu Khristu. Tiyeni tsono, tipemphe Mulungu kuti anthu onse avomere kuitana kwakeko.
1. Eklezia wa Mulungu, aonetse anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu, m’maphunziro ake, ndinso m’ntchito zake zosamalira anthu osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu onse amene sanamvebe Mthenga Wabwino, atsekulire Mulungu mitima yao, amfunefune mwakhama mpaka adzampezedi.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akulu olamulira maiko atsate ubwino wa anthu ao mopanda tsankho, ndipo awapatse ufulu weniweni pa za chipembedzo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse talandira udindo wotsogolera anzathu m’njira ya chipulumutso; kuwala kwa Yesu Khristu kuwonekere m’mayendedwe athu ndi m’zochita zathu zonse.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athuwa pamodzi ndi zosowa za anthu onse. Tikuyamika kukoma mtima kwanu kofuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment