Saturday, January 25, 2025

LAMULUNGU LA 3 PA CHAKA – C

LAMULUNGU LA 3 PA CHAKA – C

“Mau anu ndi opatsa moyo wosatha.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NEHEMIYA: NEHEMIYA 8:2-6,8-10. (Ezara adawerenga buku la Malamulo, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino).

 

Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Tsono Ezara adawerenga bukulo atayang’ana bwalo la chipata cha madzi, kuyambira m’mamawa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zowerengazo. Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Kudzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu. Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira. Kenaka Ezara adati, “atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaweramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire. Aleviwo adawerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino. Tsono bwanamkubwa Nehemiya, pamodzi ndi Ezara wansembe ndi Mphunzitsi wa malamulo, kudzanso Alevi amene ankaphunzitsa anthu, adauza anthu onse aja kuti, “lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Ndiye kuti anthu onse ankalira atamva mau a Malamulowo. Tsono Nehemiya adapititriza nati, “kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muwapetseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19:8-10, 15.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Mau a Chauta ngangwiro,

Amapatsa munthu moyo watsopano,

Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika,

Umawapatsa nzeru amene alibe.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Malangizo a Chauta ndi olungama,

Amasangalatsa mtima,

Malamulo a Chauta ndi olungama,

Amapatsa mtima womvetsa.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

Chimakhala mpaka muyaya,

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

Ncholungama nthawi zonse.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

 

Mau anga ndi maganizo anga,

Avomerezeke pamaso panu,

Inu Chauta, thanthwe langa,

Ndi Mpulumutsi wanga.

 

Mau anu ndi mzimu, Ambuye, ndipo ndi moyo.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12:12-21, 27. (Inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo).

 

Abale, Khristu ali ngati thupi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri. Nanga phazi litanena kuti, “poti sindine dzanja, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Nanga khutu litanena kuti, “poti sindine diso, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Kodi thupi lonse likadakhala diso lokha, bwenzi munthu akumva bwanji? Kapena thupi lonse likadakhala khutu lokha, bwenzi munthu akuninkhiza bwanji? Koma m’mene ziliri Mulungu adaika chiwalo chilichonse pamalo pake m’thupi, monga momwe adafunira. Ziwalo zonse zikadangokhala chiwalo chimodzi, sipakadakhala thupi konse. Komatu ziwalo nzambiri, ngakhale thupi ndi limodzi lokha. Motero diso silingauze dzanja kuti, “ndilibe nawe ntchito.” Ndiponso mutu sungauze mapazi kuti, “ndilibe nanu ntchito.” Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 4:18.

 

Alleluia, Alleluia Ambuye wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 1:1-4; 4:14-21. (Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwawamva).

 

Ateofilo olemekezeka, anthu ambiri adayesa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu. Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziwona chamaso kuyambira pachiyambi pake, nakhala akuzilalika. Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m’mene zonsezo zidaachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane. Ndatero kuti mudziwe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi. Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonseli. Ankaphunzitsa m’nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda. Nthawi ina Yesu adafika ku Nazerete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adalowa m’nyumba yamapemphero, monga adazolowera, naimirira kuti awerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikawapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthawi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m’nyumbamo ankangomupenyetsetsa. Tsono Yesu adawauza kuti, “lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvawa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tamva mau ake a Mulungu. Ifenso tsopano tikweze mau athu kwa Atate athu a Kumwamba, pozindikira zosowa zathu ndi za anthu onse:

 

1.     Tipempherere atsogoleri a Mpingo kuti apitirize kulalika Mthenga Wabwino mokondwera ndi modzipereka.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu ndi akatekumeni onse, kuti Mzimu Woyera aike m'mitima yao njala yolakalaka kumva mau a Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anthu onse amene ali m'mavuto, kuti azindikire kukoma mtima kwa Mulungu pakumva za Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe tili muno kuti tikhale okondana ndi ogwirizana pozindikira kuti tonse ndife ziwalo za thupi limodzi limene mutu wake ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, tikukuyamikani kuti mumalankhula nafe masiku onse chifukwa mau anu ndi opatsa moyo ndi olimbitsa chikhulupiriro m'mitima mwathu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, January 18, 2025

LAMULUNGU LA 2 PA CHAKA – C

LAMULUNGU LA 2 PA CHAKA – C.

“Ophunzira ake adamkhulupirira”.

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 62:1-5. (Mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi).

 

Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala, ndipo chipulumutso chake chitaoneka ngati muuni woyaka. Iwe Yerusalemu, mitundu ya anthu idzakuwona utapambana pa nkhondo, mafumu ao onse adzaona ulemerero wako. Adzakuitanira dzina latsopano, limene adzakutcha ndi Chauta yemwe. Udzakhala ngati chisoti chaufumu chokongola m’manja mwa Chauta, ngati msangamutu yaulemerero m’manja mwa Mulungu wako. Sudzatchedwanso ‘wosiyidwa’, dziko lako silidzatchedwanso ‘chipululu’. Dzina lako latsopanolo lidzakhala ‘ndikukondwera naye’. Dziko lako lidzatchedwa ‘wokwatiwa mwachimwemwe’, chifukwa choti Chauta akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako. Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96:1-3,7-10.

 

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!

Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

 

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

 

Lengezani za ulemerero wake,

Kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa,

Kwa anthu a m’maiko onse.

 

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

 

Tamandani, inu anthu a mitundu yonse,

Vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake,

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

 

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

 

Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera,

Njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi,

Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu.”

Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.

 

Lalikani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu a m’maiko onse.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12:4-11. (Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amagawira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kum’gawira).

 

Abale, pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kulankhula mau olangiza anthu. Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda. Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziwika, ndipo amapatsa wina mphatso za kutanthauzira zilankhulozo. Amene amachititsa anthu zonsezi ndi Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Amagawira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgawira.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 2 ATESALONIKA 2:14.

Alleluia, Alleluia Mulungu adakuitanani kudzera mwa Uthenga Wabwino kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 2:1-11. (Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m’mudzi wa Kana m’dera la Galileya).

 

Kunali Ukwati ku mudzi wa Kana m’dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko. Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “wawathera vinyo.” Yesu adayankha kuti, “Mai kodi mukuti nditani? Nthawi yangatu siinafike.” Apo mai ake adauza anyamata amene ankatumukira kuti, “chilichonse chimene akuuzeni, muchite.” Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M’mbiya iliyonse munkalowa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo. Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “dzadzani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzadza mpaka m’milomo. Pambuyo pake adawauza kuti, “tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa mphwando.” Iwowo adakaperekadi. Mkulu wa phwandoyo adalawa madzi osanduka vinyoyo osadziwa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziwa). Tsono mkulu wa mphwandoyo adaitana mkwati, namuuza kuti, “anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amawapatsa vinyo wokoma pang’ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.” Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m’mudzi wa Kana m’dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga Amai Maria adakhulupirira, napempha Mwana wao mosakayika, ifenso tikweze mau athu kwa Atate a Kumwamba ndi mtima wokhulupirira:

 

1.     Atate, muwongolere Mpingo wanu ndi Mzimu Woyera kuti akhale chizindikiro chosonyeza chipulumutso chanu kwa anthu a mafuko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mudzutse akhristu ofooka kuti ayambenso kulandira masakramenti anu, pozindikira kuti mwambo wa Ukaristia ndi kasupe wa moyo wonse wachikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muthandize anyamata ndi atsikana oyembekeza kumanga banja kuti azindikire ulemerero wa ukwati ndi kumakonzekeratu pakutenga makhalidwe oyenera.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, mulunzitse mitima yathu, kuti tisenze udindo wathu molimbika ndi mogwirizana, aliyense malinga ndi mphatso zimene adamninkha Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate achifundo, mverani mapemphero athuwa, popeza kuti ndife ana anu ndithu, ndipo taika chikhulupiriro chathu chonse pa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, January 11, 2025

CHAKA CHA UBATIZO WA AMBUYE YESU – C

CHAKA CHA UBATIZO WA AMBUYE YESU – C.

“Iye ndiye Mwana wanga wapamtima.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 42:1-4,6-7. (Nayu Mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye).

 

Chauta akuti, “nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankha, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo. Sadzafuula kapena kukweza mau, mau ake sadzamveka mu mseu. Bango lopindika sadzalithyola, moto wozilala sadzauzima. Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika. Sadzafookera kapena kutaya mtima, mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi. Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake. “Ine Chauta ndakuitana kuti ukhazikitse chilungamo. Ndakugwira padzanja ndi kukusunga. Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu, ukhale kuwala kounikira anthu a mitundu ina. Udzawatsekula maso athu akhungu, udzamasula akaidi m’ndende, udzatulutsa m’ndende anthu okhala mu mdima.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 29:1-4,9-10.

 

Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere

 

Tamandani Chauta, inu okhala kumwamba,

Tamandani ulemerero wake ndi mphamvu zake,

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta,

Mumpembedze mu Ulemu wa ungwiro wake.

 

Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere

 

Liwu la Chauta likumveka pamwamba pa nyanja,

Liwu lake lamveka pa nyanja yaikulu,

Liwu la Chauta ndi lamphamvu,

Liwu la Chauta ndi laulamuliro.

 

Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere

 

Liwu la Chauta likuzunguza miwanga,

Onse a m’nyumba mwake akufuula kuti, “Ulemererewo!”

Chauta amalamulira nyanja zonse,

Amakhala kwamuyaya pa mpando wake wachifumu.

 

Chauta amawadalitsa anthu ndi mtendere

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 10:34-38. (Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu).

 

Petro adayamba kulankhula, adati, “zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo. Mukudziwa kuti adatumizira Aisraele mau ake nawauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 9:7.

Alleluia, Alleluia Padafika mtambo ndipo mu mtambomo mudamveka mau a Atate akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.” Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 3:15-16,21-22. (Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka).

 

Pa nthawi yomweyo, chiyembekezo cha anthu chidayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane kuti kapena ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Tsono Yohane Ankawauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m’moto.” Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Mzimu Woyera wokhala mwa ife akutitsimikizira kuti ndifedi ana a Mulungu; tiyeni tsono tipemphe Atate athu a Kumwamba madalitso ao.

 

1.     Atsogoleri a Mpingo asenze udindo wao molimbika, podziwa kuti alikupitiriza ntchito ya Yesu Khristu pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko, Mzimu Woyera angolere nzeru zao, adziwe kulondoloza anthu a m'njira ya chilungamo ndi mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, akhale ndi mtima wosirira kusanduka nawonso ana a Mulungu ndi atumiki ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tasonkhana muno, Atate atidzaze ndi Mzimu wake wachikondi, nafenso tizichita ntchito zabwino ponseponse potsanzira Yesu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, potula mapemphero athuwa m’manja mwanu, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa mudatisandutsa ana anu ndi atumiki anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB 

CHAKA CHA EPIFANIYA – C

CHAKA CHA EPIFANIYA – C

“Yesu Mpulumutsi adadzera anthu a mitundu yonse.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 60:1-6. (Ulemerero wa Chauta udzawoneka).

 

Iwe Yerusalemu dzuka, wala, kuwala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuwalira. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuwalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Anthu a mitundu ina adzatsata kuwala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuwa limene likutuluka kumene. Yang’ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m’manja ngati ana. Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe. Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing’onozing’ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72:1-2,7-8,10-13.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,

Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,

Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,

Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo,

Mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso,

Mafumu onse adzaigwadira,

Ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,

Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,

Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,

Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 3:2-3,5-6. (Chinsinsicho nchakuti anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda).

 

Abale, kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake. Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa. Chinsinsi chimenecho anthu a mibadwo yakale sadachidziwe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake. Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 2:2.

Alleluia, Alleluia Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 2:1-12. (Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye).

 

Yesu adabadwira m’mudzi wa Betelehemu, m’dziko la Yudeya, pa nthawi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “ali kuti mwana amene adabadwa kuti akhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu onse a m’Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Tsono Herode yo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, nawafunsa kuti, “kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” Iwo adati, “M’mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti, Iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe wamng’ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri amene adzalamulira anthu anga Aisraele.” Pamenepo Herode adawaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, nawafunsitsa za nthawi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. Kenaka adawatumiza ku Betelehemu nkuwauza kuti, “pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziwitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idawatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adalowa m’nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adawachenjeza m’maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tonse taitanidwa kudzalandira chipulumutso mwa Yesu Khristu. Tiyeni tsono, tipemphe Mulungu kuti anthu onse avomere kuitana kwakeko.

 

1.     Eklezia wa Mulungu, aonetse anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu, m’maphunziro ake, ndinso m’ntchito zake zosamalira anthu osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu onse amene sanamvebe Mthenga Wabwino, atsekulire Mulungu mitima yao, amfunefune mwakhama mpaka adzampezedi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akulu olamulira maiko atsate ubwino wa anthu ao mopanda tsankho, ndipo awapatse ufulu weniweni pa za chipembedzo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse talandira udindo wotsogolera anzathu m’njira ya chipulumutso; kuwala kwa Yesu Khristu kuwonekere m’mayendedwe athu ndi m’zochita zathu zonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athuwa pamodzi ndi zosowa za anthu onse. Tikuyamika kukoma mtima kwanu kofuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu ambuye athu.


#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...