CHAKA CHA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – C
(25 DECEMBER)
“Adadzatisandutsa ana a Mulungu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 52:7-10. (Dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu).
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m’mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.” Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98:1-6.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,
Popeza kuti wachita zodabwitsa,
Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,
Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse,
Kuti Iye ndi wolungama,
Wakumbukira chikondi chake chosasinthika.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,
Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi,
Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,
Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,
Imbirani Chauta Mfumu,
Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA AHEBERI: AHEBERI 1:1-6. (Mulungu analankhula kwa ife kuchokera kwa Mwana wake).
Abale, kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake. Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala. Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia – Tsiku loyera lija latifikira ife. Bwerani inu mafuko onse, kuti timulambire Ambuye, popeza lero kuwala kwationekera pa dziko lonse lapansi. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 1:1-5, 9-14. (Mau aja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu).
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu. Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako. Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Yesu Khristu adadzatisandutsa ana a Mulungu, Iye anakhala ngati mkulu wathu. Tiyeni tsono pamodzi naye, tiyamike Atate athu ndi kupempha chithandizo chao:
1. Tipempherere atsogoleri a Mpingo kuti alimbitse chikhulupiriro cha anthu awo. Awatsimikizire kuti Yesu Khristu ndiyedi Mwana wa Mulungu wanthawi zonse. Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, ndipo aike chikhulupiriro chao chonse mwa Yesu Khristu, kuti nawonso asanduke ana ake a Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu onse amene adakali padera, osadziwa Mthenga Wabwino, Yesu Khristu awaunikire ndi kuwatsogolera ku moyo wosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse amene tidasanduka abale ake a Yesu Khristu pa Ubatizo, mau athu ndi mayendedwe athu asonyeze kuwala kwake ndi chikondi chake kwa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikuthokozani chifukwa mwa Mwana wanu wosanduka munthu, mudatizindikiritsa kukoma mtima kwanu. Mwa lyeyo tidalandira madalitso otsatanatsatana. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment