CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – C
“Adampereka Mwanayo kwa Ambuye.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 1 SAMUELE 1:20–22, 24–28. (Samuele adzakhala ku nyumba ya Mulungu moyo wake wonse).
Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “ndidachita kumpempha kwa Chauta.” Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake. Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna waku kuti, “malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.” Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng’ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogaramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng’ono ndithu, adapita nayebe. Kumeneko adapha ng’ombe yamphongo ija ndipo mwanayo adampereka kwa Eli. Tsono Hana adati, “inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta. Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho. Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 84:2-3, 5-6, 9-10.
Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.
Malo amene mumakhala, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri,
Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
Kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta,
Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.
Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu,
Namaimba nyimbo zotamanda Inu nthawi zonse,
Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu,
Amene m’mitima mwao amafunitsitsa kudzera m’misewu yopita ku Ziyoni.
Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,
Imvani pemphero langa,
Tcherani khutu, Inu Mulungu wa Yakobe,
Inu Mulungu, ndinu chishango chathu,
Yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.
Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 1 YOHANE 3:1-2, 21-24. (Timatchedwa ana a Mulungu, ndipo ndifedi ana ake).
Okondeka, onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziwa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziwe. Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziwa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu. Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa. Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira. Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziwa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AKOLOSE 3:15a, 16a
Alleluia, Alleluia – Mutsekule mtima wathu, Ambuye, kuti tilandire mau a Mwana wanu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 2:41-52. (Adampeza m’Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi).
Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Pasaka. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziwiri, iwo adapita kumeneko monga adaazolowera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziwa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu. Patapita masiku atatu, adampeza m’Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumawafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka m’Nyumba ya Atate anga?” Koma iwo sadamvetse zimene adawayankhazo. Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankawamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake. Ndipo Yesu analikunka nakula m’nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero polemekeza Banja Loyera la ku Nazarete, tiyeni, tipemphere mabanja onse a m’dziko lapansi:
1. Apapa ndi aepiskopi onse atsogolere akhristu ao pa njira ya ungwiro, aziwadziwitsa ukulu ndi ulemerero wa moyo wa banja.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko ateteze mabanja a anthu, pakukhazika malamulo olungama ndi kukweza miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Mabanja osowa mtendere, eni ake alezerane mtima, ndipo ayesetse kuyanjana ndi kupirirana, potsata chifuniro cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Anyamata ndi atsikana azindikire njira imene Mulungu akuwafunira, ndipo aitsate njirayo molimba mtima ndi mwaufulu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu wathu, tikupemphani zonsezi mosaopa ndi mosakayika, pakuti ndinu Atate a ife tonse, ndipo mumafuna kutisonkhanitsa tonse m’Banja lanu loyera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment