Tuesday, December 31, 2024

CHAKA CHA AMAI MARIA, MAI A MULUNGU – C

CHAKA CHA AMAI MARIA, MAI A MULUNGU – C

“Adabadwa mwa Virgo Maria.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NUMERI: NUMERI 6:22-27 (Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi).

 

Chauta adauza Mose kuti, “uza Aroni ndi ana ake kuti azidalitsa Aisraele motere: Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni.  Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.” Ndipo Chauta adati, “Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzaŵadalitsadi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67:2-3,5,6,8.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

Mutiwunikire ndi chikondi chanu,

Njira yanu idziwike pa dziko lonse lapansi,

Chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,

Ndi kuwatsogolera pa dziko lapansi.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

Inde, Mulungu watidalitsa,

Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AGALATIYA: AGALATIYA 4:4-7 (Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi).

 

Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!” Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mloŵachuma wake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AHEBERI 1:1-2

Alleluia, Alleluia Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 2:16-21 (Adampeza Maria ndi Yosefe ndi Mwanayo ... Pamene tsiku lachisanu ndi chitatu linakwana anampatsa mwanayo dzina loti Yesu).

 

Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m’chodyera cha zoŵeta chija.  Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo.  Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankaŵasimbira.  Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake.  Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.  Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, pamodzi ndi Virgo Maria, Amai a Mulungu ndi Amai athu, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti adalitse anthu onse ndi kuwatsogolera m'njira ya chipulumutso.

 

1.     Akhristu onse azindikire ulemerero wa Virgo Maria ndinso udindo wake wa Mai wotiperekeza kwa Mwana wake Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu a mafuko onse akhale oyanjana ndi ogwirizana mwaubale, ndipo choncho mtendere weniweni ukhazikike pakati pa maiko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu onse amene tikuwakonda, makamaka odwala ndi onse osowa chithandizo, tiziwaonetsa mtima wachifundo pakuwachitira zokoma.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino tikhale odziwa kuthokoza Mulungu masiku onse, polingalira m'mitima mwathu zazikulu zimene Ambuye amatichitira.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, landirani mapemphero athuwa pamodzi ndi mafuno a anthu onse. Mutisunge tonse m'chikondi chanu pa masiku onse a chaka chino. Mwa Yesu Khristu ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, December 28, 2024

CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – C

CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – C

 “Adampereka Mwanayo kwa Ambuye.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 1 SAMUELE 1:20–22, 24–28. (Samuele adzakhala ku nyumba ya Mulungu moyo wake wonse).

 

Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “ndidachita kumpempha kwa Chauta.” Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake. Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna waku kuti, “malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.” Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng’ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogaramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng’ono ndithu, adapita nayebe. Kumeneko adapha ng’ombe yamphongo ija ndipo mwanayo adampereka kwa Eli. Tsono Hana adati, “inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta. Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho. Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 84:2-3, 5-6, 9-10.

 

Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.

 

Malo amene mumakhala, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri,

Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,

Kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta,

Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.

 

Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.

 

Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu,

Namaimba nyimbo zotamanda Inu nthawi zonse,

Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu,

Amene m’mitima mwao amafunitsitsa kudzera m’misewu yopita ku Ziyoni.

 

Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.

 

Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

Imvani pemphero langa,

Tcherani khutu, Inu Mulungu wa Yakobe,

Inu Mulungu, ndinu chishango chathu,

Yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.

 

Ngodala anthu amene amakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 1 YOHANE 3:1-2, 21-24. (Timatchedwa ana a Mulungu, ndipo ndifedi ana ake).

 

Okondeka, onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziwa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziwe. Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziwa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu. Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa. Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira. Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziwa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AKOLOSE 3:15a, 16a

Alleluia, Alleluia Mutsekule mtima wathu, Ambuye, kuti tilandire mau a Mwana wanu. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 2:41-52. (Adampeza m’Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi).

 

Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Pasaka. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziwiri, iwo adapita kumeneko monga adaazolowera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziwa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu. Patapita masiku atatu, adampeza m’Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumawafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka m’Nyumba ya Atate anga?” Koma iwo sadamvetse zimene adawayankhazo. Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankawamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake. Ndipo Yesu analikunka nakula m’nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, lero polemekeza Banja Loyera la ku Nazarete, tiyeni, tipemphere mabanja onse a m’dziko lapansi:

1.     Apapa ndi aepiskopi onse atsogolere akhristu ao pa njira ya ungwiro, aziwadziwitsa ukulu ndi ulemerero wa moyo wa banja.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko ateteze mabanja a anthu, pakukhazika malamulo olungama ndi kukweza miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Mabanja osowa mtendere, eni ake alezerane mtima, ndipo ayesetse kuyanjana ndi kupirirana, potsata chifuniro cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Anyamata ndi atsikana azindikire njira imene Mulungu akuwafunira, ndipo aitsate njirayo molimba mtima ndi mwaufulu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu wathu, tikupemphani zonsezi mosaopa ndi mosakayika, pakuti ndinu Atate a ife tonse, ndipo mumafuna kutisonkhanitsa tonse m’Banja lanu loyera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Tuesday, December 24, 2024

CHAKA CHA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – C

CHAKA CHA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – C

(25 DECEMBER)

“Adadzatisandutsa ana a Mulungu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 52:7-10. (Dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu).

 

Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m’mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”  Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98:1-6.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,

Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse,

Kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi,

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,

Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,

Imbirani Chauta Mfumu,

Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA AHEBERI: AHEBERI 1:1-6. (Mulungu analankhula kwa ife kuchokera kwa Mwana wake).

 

Abale, kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake. Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala. Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO

Alleluia, Alleluia Tsiku loyera lija latifikira ife. Bwerani inu mafuko onse, kuti timulambire Ambuye, popeza lero kuwala kwationekera pa dziko lonse lapansi. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 1:1-5, 9-14. (Mau aja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu).

 

Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.  Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu. Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako. Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu Khristu adadzatisandutsa ana a Mulungu, Iye anakhala ngati mkulu wathu. Tiyeni tsono pamodzi naye, tiyamike Atate athu ndi kupempha chithandizo chao:

1.     Tipempherere atsogoleri a Mpingo kuti alimbitse chikhulupiriro cha anthu awo. Awatsimikizire kuti Yesu Khristu ndiyedi Mwana wa Mulungu wanthawi zonse. Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, ndipo aike chikhulupiriro chao chonse mwa Yesu Khristu, kuti nawonso asanduke ana ake a Mulungu.

Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu onse amene adakali padera, osadziwa Mthenga Wabwino, Yesu Khristu awaunikire ndi kuwatsogolera ku moyo wosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.


4.     Ife tonse amene tidasanduka abale ake a Yesu Khristu pa Ubatizo, mau athu ndi mayendedwe athu asonyeze kuwala kwake ndi chikondi chake kwa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikuthokozani chifukwa mwa Mwana wanu wosanduka munthu, mudatizindikiritsa kukoma mtima kwanu. Mwa lyeyo tidalandira madalitso otsatanatsatana. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.


#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Monday, December 23, 2024

CHAKA CHA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – C

CHAKA CHA KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – C

(MISA YA USIKU – 24 DECEMBER).

“Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 9:1-7. (Mwana watibadwira).

 

Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Aneneratu za mfumu yamtsogolo. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuwala kwakukulu. Amene ankakhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo Akukondwa pamaso panu monga m’mene anthu amakondwera nthawi ya masika, monganso m’mene anthu amakondwera pogawana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkawalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewera ao, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani. Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m’manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “phungu wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide., ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96:1-3, 11-13.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi,

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku,

Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m’maiko onse.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere,

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Mitengo yankhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta,

Pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo,

Adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA TITO: TITO 2:11-14. (Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse).

 

Abale, Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 2:10-11.

Alleluia, Alleluia Ndadzakuuzani za uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 2:1-14. (Lero Mpulumutsi watibadwira).

 

Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m’maiko ake onse. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazerete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi la Davideyo. Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Pamene anali kumeneko, nthawi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m’nsalu namgoneka m’chodyera cha zoweta, chifukwa adaasowa malo m’nyumba ya alendo. Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoweta zao ku dambo usiku. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udawala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo adawauza kuti, “musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m’mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m’chodyera cha zoweta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pamodzi ndi Yesu Khristu amene adadzakhala munthu m’nzathu kuti atitsogolere kwa Atate ake, tiyeni tipemphe madalitso a Mulungu pa ife ndi pa anthu onse.

1.     Tipempherere Eklezia wa Mulungu, kuti apitirize kuunikira anthu onse pakuwaonetsa kukoma mtima kwa Mulungu kofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu amene adakali m’mdima, osadziwa mthenga wabwino wa pa Khrisimasi, maso awo akopedwe, poona m’mene akhristu amakonderana.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Ana onse obadwira m’dziko lino lapansi alandire chikondi ndi chisamaliro chokwanira kuchokera kwa makolo ao, ndipo choncho akule ndi moyo wabwino.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’parish yathu ino, moyo wathu ukhale wochitira Mulungu ulemu ndi wodzetsa mtendere ndi chimwemwe m’mitima ya anzathu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, ife tonse ana anu tikuyamika chifundo chanu chosaneneka, chifukwa mudatidalitsa koposa, pakutipatsa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...