Sunday, December 31, 2023

CHAKA CHA MARIA WOYERA, AMAI A MULUNGU

CHAKA CHA MARIA WOYERA, AMAI A MULUNGU – B

“Adabadwa mwa Virgo Maria.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NUMERI; NUMERI 06: 22 – 27. (Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi).

 

Chauta adauza Mose kuti, “uza Aroni ndi ana ake kuti azidalitsa Aisraele motere: Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang’aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima.

Chauta akuyang’aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.” Ndipo Chauta adati, “akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 02 – 03, 05 – 06, 08.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

Mutiwunikire ndi chikondi chanu,

Njira yanu idziwike pa dziko lonse lapansi,

Chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,

Ndi kuwatsogolera pa dziko lapansi.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

Inde, Mulungu watidalitsa,

Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze lye.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

------------------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AGALATIYA; AGALATIYA 04: 04 – 07. (Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi).

 

Abale, nthawi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m’mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, ‘Abba! Atate!’ Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mlowachuma wake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AHEBRI 01: 01 – 02.

Alleluia, Alleluia – Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 02: 16 – 21. (Adampeza Maria ndi Yosefe ndi Mwanayo …Pamene tsiku la chisanu ndi chitatu linakwana anampatsa mwanayo dzina loti Yesu).

 

Abusa adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m’chodyera cha zoweta chija. Pamene adamuwona, abusawo adawafotokozera zimene mngelo uja adaawauza za mwanayo. Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankawasimbira. Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaawauzira. Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pamodzi ndi Virgo Maria, Amai a Mulungu ndi Amai athu, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti adalitse anthu onse ndi kuwatsogolera m’njira ya chipulumutso.

 

1.     Akhristu onse azindikire ulemerero wa Virgo Maria ndinso udindo wake wa Mai wotiperekeza kwa Mwana wake Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu a mafuko onse akhale oyanjana ndi ogwirizana mwaubale, ndipo choncho mtendere weniweni ukhazikike pakati pa maiko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu onse amene tikuwakonda, makamaka odwala ndi onse osowa chithandizo, tiziwaonetsa mtima wachifundo pakuwachitira zokoma.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino tikhale odziwa kuthokoza Mulungu masiku onse, polingalira m’mitima mwathu zazikulu zimene Ambuye amatichitira.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, landirani mapemphero athuwa pamodzi ndi mafuno a anthu onse. Mutisunge tonse m’chikondi chanu pa masiku onse a chaka chino. Mwa Yesu Khristu ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, December 30, 2023

CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – CHAKA B

CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – CHAKA B.

“Adapereka mwanayo kwa Ambuye.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 15: 01 – 06; 21: 01 – 03. (Uyu sadzalandira chuma chako kukhala cholowa chake).

 

Chauta adaonekera Abramu m’masomphenya namuuza kuti, “usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Wolowa m’malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu. Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale cholowa chake.” Tsono Chauta adamuuza kuti, “uyu sadzalandira chuma chako kukhala cholowa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.” Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “tayang’ana kuthamboku, ndipo uwerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” Apo Abramu adakhulupilira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama. Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza. Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali khalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthawi yeniyeni imene Mulungu adaanena. Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 105: 01 – 06, 08 – 09.

 

Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.

 

Thokozani Chauta, tamandani dzina lake,

Lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda,

Lalikani za ntchito zake zodabwitsa.

 

Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.

 

Mudyadire dzina lake loyera,

Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta,

Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake,

Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.

 

Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.

 

Inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,

Ana a Yakobe, osankhidwa ake,

Musaiwale ntchito zodabwitsa ndi zozizwitsa zimene ankazichita,

Ndiponso m’mene ankaweruzira anthu.

 

Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.

 

Amasunga chipangano chake nthawi zonse,

Sangaiwale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse,

Amasunga chipangano chimene adachita ndi Abrahamu,

Lonjezo lake limene adapatsa Isaki molumbira.

 

Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBERI; AHEBERI 11: 08, 11 – 12, 17 – 19. (Chikhulupiliro cha Abraham, Sara ndi Isaki).

 

Abale, pokhala ndi chikhulupiliro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamulonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziwa kumene ankapita, adapitabe. Pokhala ndi chikhulupiliro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika. Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosawerengeka ngati mchenga wa gombe la nyanja. Pokhala ndi chikhulupiliro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. Za mwana ameneyu Mulungu anali atanena kuti, ‘mwa Isaki udzakhala ndi zidzukulu.’ Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AHEBRI 01: 01 – 02.

 

Alleluia, Alleluia – Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 02: 22 – 40. (Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru).

 

Kenaka idafika nthawi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayi adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye. Pajatu m’Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.” Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “apereke njiwa ziwiri kapena maunda awiri.” Ku Yerusalemu kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adalowanso m’Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m’manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Ndimaso angawa ndachiwonadi chipulumutso chija, chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone. Mwapereka kuwala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.” Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za Mwanayo. Kenaka Simeoniyo adawadalitsa, nauza Maria, mai wa Mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho, kuti choncho maganizo amene ali m’mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.” Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziwiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya. Iye adafikako nthawi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu. Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, lero polemekeza Banja Loyera la ku Nazarete, tiyeni, tipemphere mabanja onse a m’dziko lapansi.

 

1.     Apapa ndi Aepiskopi onse atsogolere akhristu ao pa njira ya ungwiro, aziwadziwitsa ukulu ndi ulemerero wa moyo wa banja.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko ateteze mabanja a anthu, pakukhazika malamulo olungama ndi kukweza miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Mabanja osowa mtendere, eni ake alezerane mtima, ndipo ayesetse kuyanjana ndi kupirirana, potsata chifuniro cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Anyamata ndi atsikana azindikire njira imene Mulungu akuwafunira, ndipo aitsate njirayo molimba mtima ndi mwaufulu.

Tikupemphani, mutivomereze.


Mulungu wathu, tikupemphani zonsezi mosaopa ndi mosakayika, pakuti ndinu Atate a ife tonse, ndipo mumafuna kutisokonkhanitsa tonse m’Banja lanu loyera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Sunday, December 24, 2023

KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA B [MISA YA MASANA]

KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA B

[MISA YA MASANA]

“Adadzatisandutsa ana a Mulungu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 52: 07 – 10. (Dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu).

 

Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m’mapiri, kubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu. Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta wawatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 01 – 06.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,

Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,

Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi.

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,

Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,

Imbirani Chauta Mfumu,

Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBERI; AHEBERI 01: 01 – 06. (Mulungu analankhula kwa ife kuchokera kwa Mwana wake).

 

Abale, kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati cholowa chake. lye ndiye kuwala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuwachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake kale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.” Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 01: 01 – 18.

Alleluia, Alleluia – Tsiku loyera lija latifikira ife. Bwerani inu mafuko onse, kuti timulambire Ambuye, popeza lero kuwala kwationekera pa dziko lonse lapansi. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 01: 01 – 05, 09 – 14. (Mau aja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu).

 

Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa lyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu. Kuwalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuwalako. Kuwala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m’dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa lye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu,

koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo amenewa lye adawapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m’kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu Khristu adadzatisandutsa ana a Mulungu, Iye anakhala ngati mkulu wathu. Tiyeni tsono pamodzi naye, tiyamike Atate athu ndi kupempha chithandizo chao:

 

1.     Tipempherere atsogoleri a Mpingo kuti alimbitse chikhulupiriro cha anthu awo. Awatsimikizire kuti Yesu Khristu ndiyedi Mwana wa Mulungu wanthawi zonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, ndipo aike chikhulupiriro chao chonse mwa Yesu Khristu, kuti nawonso asanduke ana ake a Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu onse amene adakali padera, osadziwa Mthenga Wabwino, Yesu Khristu awaunikire ndi kuwatsogolera ku moyo wosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse amene tidasanduka abale ake a Yesu Khristu pa Ubatizo, mau athu ndi mayendedwe athu asonyeze kuwala kwake ndi chikondi chake kwa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikuthokozani chifukwa mwa Mwana wanu wasanduka munthu, mudatizindikiritsa kukoma mtima kwanu. Mwa Iyeyo tidalandira madalitso otsatanatsatana. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/ 

KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA B [MISA YA USIKU]

KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA B

[MISA YA USIKU]

“Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 09: 01 – 07. (Mwana watibadwira).

 

Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Aneneratu za mfumu yam’tsogolo. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuwala kwakukulu. Amene ankakhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m’mene anthu amakondwera nthawi ya masika, monganso m’mene anthu amakondwera pogawana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkawalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani. Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m’manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01 – 03, 11 – 13.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku,

Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m’maiko onse.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere,

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Mitengo yam’nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta,

Pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo,

Adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA TITO; TITO 02: 11 – 14. (Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse).

 

Abale, Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja lye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 02:10 – 11.

Alleluia, AlleluiaNdadzakuuzani za uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 02: 01 – 14. (Lero Mpulumutsi watibadwira).

 

Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m’maiko ake onse. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi fuko la Davideyo. Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Pamene anali kumeneko, nthawi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m’nsalu namgoneka m’chodyera cha zoweta, chifukwa adaasowa malo m’nyumba ya alendo. Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoweta zao ku dambo usiku. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udawala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo adawauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m’mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m’chodyera cha zoweta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pamodzi ndi Yesu Khristu amene adadzakhala munthu m’nzathu kuti atitsogolere kwa Atate ake, tiyeni tipemphe madalitso a Mulungu pa ife ndi pa anthu onse.

 

1.     Tipempherere Eklezia wa Mulungu, kuti apitirize kuunikira anthu onse pakuwaonetsa kukoma mtima kwa Mulungu kofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu amene adakali m’mdima, osadziwa mthenga wabwino wa pa Khrisimasi, maso awo akopedwe, poona m’mene akhristu amakonderana.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Ana onse obadwira m’dziko lino lapansi alandire chikondi ndi chisamaliro chokwanira kuchokera kwa makolo ao, ndipo choncho akule ndi moyo wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’parish yathu ino, moyo wathu ukhale wochitira Mulungu ulemu ndi wodzetsa mtendere ndi chimwemwe m’mitima ya anzathu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, ife tonse ana anu tikuyamika chifundo chanu chosaneneka. chifukwa mudatidalitsa koposa, pakutipatsa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...