CHAKA CHA BANJA LOYERA LA YESU, MARIA NDI YOSEFE – CHAKA B.
“Adapereka mwanayo kwa Ambuye.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 15: 01 – 06; 21: 01 – 03. (Uyu sadzalandira chuma chako kukhala cholowa chake).
Chauta adaonekera Abramu m’masomphenya namuuza kuti, “usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Wolowa m’malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu. Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale cholowa chake.” Tsono Chauta adamuuza kuti, “uyu sadzalandira chuma chako kukhala cholowa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.” Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “tayang’ana kuthamboku, ndipo uwerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” Apo Abramu adakhulupilira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama. Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza. Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali khalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthawi yeniyeni imene Mulungu adaanena. Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 105: 01 – 06, 08 – 09.
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake,
Lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda,
Lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.
Mudyadire dzina lake loyera,
Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta,
Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake,
Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.
Inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
Ana a Yakobe, osankhidwa ake,
Musaiwale ntchito zodabwitsa ndi zozizwitsa zimene ankazichita,
Ndiponso m’mene ankaweruzira anthu.
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.
Amasunga chipangano chake nthawi zonse,
Sangaiwale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse,
Amasunga chipangano chimene adachita ndi Abrahamu,
Lonjezo lake limene adapatsa Isaki molumbira.
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amasunga chipangano chake nthawi zonse.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBERI; AHEBERI 11: 08, 11 – 12, 17 – 19. (Chikhulupiliro cha Abraham, Sara ndi Isaki).
Abale, pokhala ndi chikhulupiliro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamulonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziwa kumene ankapita, adapitabe. Pokhala ndi chikhulupiliro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika. Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosawerengeka ngati mchenga wa gombe la nyanja. Pokhala ndi chikhulupiliro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. Za mwana ameneyu Mulungu anali atanena kuti, ‘mwa Isaki udzakhala ndi zidzukulu.’ Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AHEBRI 01: 01 – 02.
Alleluia, Alleluia – Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 02: 22 – 40. (Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru).
Kenaka idafika nthawi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayi adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye. Pajatu m’Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.” Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “apereke njiwa ziwiri kapena maunda awiri.” Ku Yerusalemu kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adalowanso m’Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m’manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Ndimaso angawa ndachiwonadi chipulumutso chija, chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone. Mwapereka kuwala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.” Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za Mwanayo. Kenaka Simeoniyo adawadalitsa, nauza Maria, mai wa Mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho, kuti choncho maganizo amene ali m’mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.” Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziwiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya. Iye adafikako nthawi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu. Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero polemekeza Banja Loyera la ku Nazarete, tiyeni, tipemphere mabanja onse a m’dziko lapansi.
1. Apapa ndi Aepiskopi onse atsogolere akhristu ao pa njira ya ungwiro, aziwadziwitsa ukulu ndi ulemerero wa moyo wa banja.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko ateteze mabanja a anthu, pakukhazika malamulo olungama ndi kukweza miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Mabanja osowa mtendere, eni ake alezerane mtima, ndipo ayesetse kuyanjana ndi kupirirana, potsata chifuniro cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Anyamata ndi atsikana azindikire njira imene Mulungu akuwafunira, ndipo aitsate njirayo molimba mtima ndi mwaufulu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu wathu, tikupemphani zonsezi mosaopa ndi mosakayika, pakuti ndinu Atate a ife tonse, ndipo mumafuna kutisokonkhanitsa tonse m’Banja lanu loyera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment