Saturday, March 26, 2022



LAMULUNGU LA 04 MU LENTI - C

(Tibwerere kwa Mulungu Atate athu.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA YOSWA: YOSWA 05: 09 – 12 (Pamene Aisraele anali m’zithando ku Giligala m’chigwa cha ku Yeriko, adachita Pasaka madzulo)

Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “lero ndakuchotserani manyazi a ukapolo wanu uja umene munali nawo ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adawatcha Giligala, ndipo mpaka lero lino malo amenewa akudziwika ndi dzina limeneli. Pamene Aisraele anali m’zithando ku Giligala m’chigwa cha ku Yeriko, adachita Pasaka madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. M’mawa mwake mpamene anthu aja adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Adakazinga tirigu, naphikanso buledi wosatupitsa tsiku limenelo. Zitangotero, mana uja adaleka kugwa, ndipo sadapezekenso pakati pa Aisraele. Kuyambira nthawi imeneyo adayamba kudya chakudya cha ku Kanani.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34: 02 – 07.

Tiyeni kwa Mulungu ndipo tidzaona kuti ndi wabwino.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse.

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza.

Moyo wanga umanyadira Chauta.

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Tiyeni kwa Mulungu ndipo tidzaona kuti ndi wabwino.

 

Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta,

Tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.

Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha.

Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.

 

Tiyeni kwa Mulungu ndipo tidzaona kuti ndi wabwino.

 

Ozunzikawo atayang’ana kwa Chauta,

Nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi.

Munthu wosaukayu adalira, ndipo Chauta adamumva,

Nampulumutsa m’mavuto ake onse.


Tiyeni kwa Mulungu ndipo tidzaona kuti ndi wabwino.


MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 05: 17 – 21 (Mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi.)

Abale, ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osawawerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiwalalike. Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m’dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 15: 18.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

Ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti; “Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe.”

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu!

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 15: 01 – 03, 11 – 32. (Mng’ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo.)

Anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake. Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuwinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” Tsono Yesu adawaphera fanizo ili, adati, “Munthu wina adaali ndi ana aamuna awiri, wamng’ono adapempha bambo wake kuti. ‘Atate, bwanji mugawiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adawagawiradi ana ake aja chuma chake. Patangopita masiku owerengeka wamng’ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa. Chitamthera chuma chake chonse, mudalowa njala yaikulu m’dziko limeneli, mwakuti iye yemwe adayamba kusauka. Pamenepo adapita kukakhala nao kwa nzika ina ya m’dzikomo. Nzikayo idamtuma ku busa kukaweta nkhumba zake. Mnyamata uja ankalakalaka kudya makoko amene nkhumba zinkadya, koma panalibe munthu wompatsako ngakhale makokowo. Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala. Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’ Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti ‘thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang’ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka: Ndiye pompo chikondwerero chidayamba. Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina. Adaitana wantchito mmodzi namufunsa kuti, ‘kodi kwagwanji?' Iye adati, Mng’ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo. Atamva zimenezo mwana wamkuluyo adapsa mtima, nakana kulowa. Apo bambo wake adatuluka, nkumupempha mopemba kuti alowe. Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga. Koma mwana wanuyu, chuma chanu chonse adaonongera akazi achiwerewere, ndipo pamene wabwera, mwamuphera mwanawang’ombe wonenepa uja!’ Bambo wakeyo adamuyankha kuti, ‘mwana wanga, iwe uli ndi ine nthawi zonse, ndipo zanga zone nzako. Kunayenera kuti tikondwere ndi kusangalala, chifukwa mng’ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, March 19, 2022




LAMULUNGU LA 03 MU LENTI – C

(Mtengo wosabereka adzaudula.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA EKSODO: EKSODO 03: 01 –08. 1 3 – 15 (NDILIPO wandituma.)

Mose ankaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina adatenga ziwetozo, nayenda nazo chakuzambwe kwa chipululu, mpaka kukafika ku phiri la Mulungu dzina lake Horebu. Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malawi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto lawilawi, koma osapsa. Tsono mumtima mwake adati, “ndipita pafupi, kuti ndikaonetsetse zozizwitsa ndikupenyazi. Chifukwa chiyani chitsambacho sichilikupsa?” Chauta ataona kuti Mose akuyandikira, adamuitana m'chitsambamo kuti, “Mose, Mose!” Mose adayankha kuti, “wawa.” Mulungu adati, “usayandikire pafupi. Vula nsapato zakozo, chifukwa malo waimapowo ngoyera.” Adapitirira kunena kuti. “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobo.” Pompo Mose adadziphimba kumaso chifukwa adaopa kupenya Mulungu. Kenaka Chauta adati, “ndaona m’mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuwapsinja. Ndikudziwa bwino kuzunzika kwao. Ndabwera kuti ndiwapulumutse kwa Aejipito ndi kuwatulutsa m’dziko limenelo, kuti ndikawalowetse m’dziko lalikulu lachonde. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Amene akukhala m’dziko limenelo ndi Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.” Mose adayankha kuti, “tsono ine ndikapita kwa Aisraelewo kukawauza kuti Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu, iwowo akakandifunsa kuti, ‘dzina lake ndani?’ Ndiye ineyo ndikawauze chiyani?” Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukawauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.” Ndipo Mulungu adamuuzanso Mose kuti, “Aisraele ukawauze kuti, Chauta, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobo, ndiye amene wandituma kwa inu. Tsono limeneli ndilo dzina langa mpaka muyaya. Limeneli ndilo dzina limene idzanditchula mibadwo yonse yam’tsogolo.”

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 06 – 8. 11.


Chauta ndi wokoma mtima ndi wachikondi.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachikondi.

 

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,

Ndi kuchiritsa matenda ako onse.

Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda.

Amakuveka chikondi chake chosasinthika,

Ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachikondi.

 

Chauta amaweruza mwachilungamo one opsinjidwa,

Amawachitira zolungama.

Adadziwitsa Mose njira zake,

Adaonetsa Aisraele ntchito zake.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachikondi.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima,

Ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu.

Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,

Ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika

Kwa anthu oopa Chauta.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachikondi.


MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 10: 01 – 06, 10 – 12 (Moyo umene makolo athu amakhala pansi pa ulamuliro wa Mose, zidalembedwa kuti tipezepo phunziro ifeyo.)

Abale, ndifuna kuti mudziwe zimene zidawachitikira makolo athu akale aja. Onse adayenda mu mthunzi wa mtambo, ndipo onse adaoloka Nyanja Yofiira. Motero mumtambomo ndi n’nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose. Onse ankadya chakudya chauzimu chimodzimodzi. Onse ankamwanso chakumwa chauzimu chimodzimodzi, pakuti analikumwa m’thanthwe lauzimu limene linkawatsatira. Thanthwelo linali Khristu yemwe. Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu. Tsono zimene zidachitikazi ndi zitsanzo zotichenjeza ife, kuti tisamasirira zoipa monga adaachitira iwowo. Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa. Zonsezi zidawagwera makolo athuwo kuti zikhale zowachenjeza. Ndipo zidalembedwa kuti tipezepo phunziro ifeyo, amene tikuyandikira nthawi ya kutha kwa zonse. Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYU 04: 17

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

'"Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira."

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 13: 01 – 09. (Mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.)

Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu. Tsono Yesu adawafunsa kuti, “Kodi mukuyesa kuti Agalileyawo anali ochimwa koposa Agalileya ena onse, popeza kuti adaphedwa motere? Iyai. koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja. Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idawagwera ku Siloamu nkuwapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m’Yerusalemu? Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.” Yesu adawaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m’munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza. Tsono adauza wosamala mundawo kuti, ‘papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’ Koma iye adati. ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa. Ukadzabala zipatso chaka chamawa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’” 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, March 12, 2022

Lamulungu Lachiwiri mu nyengo ya Lenti - Chaka C

 


LAMULUNGU LA 02 MUNYENGO YA LENTI - C

“Opanda mtanda, palibe moyo wosatha.”

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 15: 05 - 12. 17 – 18. (Mulungu adachita pangano ndi Abrahamu, Tate wa chikhulupiriro)

Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “tayang’ana kuthamboku, ndipo uwerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziwe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?” Chauta adamuyankha kuti, “tandipatsa ng'ombe ya zaka zitatu, mbuzi ya zaka zitatu, nkhosa ya zaka zitatu, ndiponso njiwa ndi nkhunda.” Abramu adabwera nazo nyama zonsezo kwa Mulungu, naziduladula pakati. Adaika mabanduwo awiriawiri mopenyanapenyana, m’mizere iwiri. Koma mbalame zija sadazidule. Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa. Pamene dzuwa linkalowa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri. Dzuwa litangolowa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziwirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija. Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.”

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 27: 01. 07 – 09.13 – 14.

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.


Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa,

Ndidzaopa yani?

Chauta ndiye linga la moyo wanga,

Nanga ndichitirenji mantha?

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula,

Mundikomere mtima ndi kundiyankha,

Pajatu Inu mudati, “muzifunafuna nkhope yanga.”

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu,

Musandibisire nkhope yanu,

Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya,

Inu amene mwakhala mukundithandiza.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.


Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta,

m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta,

Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima,

Ndithu, khulupirira Chauta.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 03: 17 – 04: 01 (Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabewa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero.)

Abale anga, nonse pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo muziwapenyetsetsa amene amayenda motsata chitsanzo chimene ife timakupatsani. Ndakhala ndikukuuzani kawirikawiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha. Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabewa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse. Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Mumandisangalatsa ndipo ndinu mphotho yanga imene ndimainyadira. Okondedwa anga, limbikani choncho mogwirizana ndi Ambuye.

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYU 17: 05.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 09: 28 – 36 (Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika.)

Patapita ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Yesu adatenga Petro, Yohane ndi Yakobo, nakwera nawo ku phiri kukapemphera. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthawi yomweyo anthu awiri adayamba kucheza naye; anali Mose ndi Eliya. Maonekedwe ao anali aulemerero, ndipo ankakambirana za imfa ya Yesu imene ankayenera kukafera ku Yerusalemu. Nthawi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m’tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu awiri aja ali naye. Pamene iwo aja ankalekana naye, Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” (Sankadziwa zimene ankanena.) Akulankhula choncho, padafika mtambo nuwaphimba, ndipo ophunzirawo adagwidwa ndi mantha. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndidamsankha, muzimumvera.” Mauwo atamveka choncho, ophunzira aja adaona kuti Yesu ali yekha. Iwo adangokhala chete masiku amenewo, osauza wina aliyense zimene adaaziwonazo.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, March 5, 2022


LAMULUNGU LA 01 MU NYENGO YA LENTI - C

“Yesu Khristu atipatsa mphamvu zogonjetsera zoipa.”

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO: DEUTERONOMO 26: 04 – 10. (Zikhulupiriro za anthu olonjezedwa.)

 

Mose adauza anthu ake kuti, “Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu. Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, ‘Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu. Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo. Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo. Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri. Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji. Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.’ Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo.”

 

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 91: 01 – 02,10 – 15.

 

Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.

 

Munthu amene amakhala m’linga la Wopambanazonse,

Iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,

Adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothawira kwanga,

ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

 

Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.

 

Zoipa sizidzakugwera,

Zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako,

Chauta adzapatsa angelo ake,

Ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.

 

Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.

 

Adzakunyamula m' manja mwao,

kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala,

Udzatha kuponda mkango ndi njoka,

Zoonadi udzaponda ndi phazi lako,

Msona wa mkango ndiponso chinjoka.

 

Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.

 

Pakuti amene amandikangamira, Ine Mulungu,

Mwachikondi, ndidzampulumutsa.

Ndidzamteteza popeza kuti amadziwa dzina langa.

Akadzandiitana, ndidzamuyankha,

Ndidzakhala naye pa nthawi yamavuto,

Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

 

Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.

 

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 10: 08 – 13. (Zikhulupiriro za Akhristu.)

 

Abale, Malembo akuti chiyani? Akuti, ‘Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.’ Amenewa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timawalalika. Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka. Paja Malembo akuti, ‘Munthu aliyense wokhulupirira lye, sadzachita manyazi.’ Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa moolowa manja onse otama dzina lake mopemba. Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, ‘Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.’

 

Mau a Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04: 04b.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

 

Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha,

koma ndi mau onse olankhula Mulungu.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 04: 01 – 13. (Mzimu Woyera yo ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa.)

 

Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala. Tsono Satana adamuuza kuti, “ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.” Koma Yesu adati. “Malembo akuti, ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha.’ Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang'ono adamuwonetsa maiko a mafumu onse a pansi pano. Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo ndimazipatsa aliyense amene ndifuna. Choncho mukandipembedza, zonsezi zidzakhala zanu.” Apo Yesu adati, “Malembo akuti, Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uziwatumikira Iwo okha.” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni ndiponso, Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, Usawayese Ambuye, Mulungu wako.” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthawi ina.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Tuesday, March 1, 2022

  

TSIKU LA PHULUSA – CHAKA  A, B, C

(Ino ndi nthawi yoti tiyanjanenso ndi Mulungu)

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YOWELE: YOWELE 02: 12 – 18. (Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu chabe)

Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwerani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu chabe. Bwerani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthawi zonse ndi wokonzeka kukhululuka. Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu. Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitane msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m’chipinda mwao, abwere. Ansembe azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena awanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asawaseke pomafunsana kuti, ‘ha, ali kuti Mulungu waoyo?”’ Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adawachitira chifundo anthu ake.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 03 – 06, 12 – 13.

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika,

Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu,

Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga,

Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

Zolakwa zanga ndikuzidziwa,

Kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthawi zonse,

Ndachimwira Inu, Inu nokha,

Ndachita choipa pamaso panu.

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,

Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,

Musandipirikitse pamaso panu,

Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,

Mulimbitse mwa ine mtima womvera,

Ambuye, tsekulani milomo yanga,

Ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO:  2 AKORINTO 05: 20 – 06: 02. (Muvomere kuyanjananso ndi Mulungu… Pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima)

Abale, ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwina ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m’dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. Paja Mulungu akuti, “pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthawi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi lerotu tsiku la chipulumutso.

 Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 95:08.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,

Ndipo mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu.

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 06: 01 – 06, 16 – 18. (Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho)

Yesu adati, “chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba. Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m’nyumba zamapemphero ndiponso m’misewu yam’mizinda. Iwowa amachita zimenezo kuti anthu awatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziwa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m’nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu ya m’mizinda. Amachita zimenezo kuti anthu awaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, lowa m’chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...