LAMULUNGU LA 01 MU NYENGO YA LENTI - C
“Yesu Khristu atipatsa mphamvu zogonjetsera zoipa.”
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA:
MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO: DEUTERONOMO 26: 04 – 10. (Zikhulupiriro za
anthu olonjezedwa.)
Mose adauza
anthu ake kuti, “Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika
patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu. Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu
wanu, muzidzanena kuti, ‘Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda,
amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko,
anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu
ndi wamphamvu. Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito
mwaukapolo. Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti
atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa
imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo. Mwa mphamvu
zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku
Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa
zambiri. Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko
lamwanaalirenji. Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola
zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.’ Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa
Mulungu, mumpembedze pomwepo.”
Mau a
Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 91:
01 – 02,10 – 15.
Mukhale nane,
Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Munthu amene
amakhala m’linga la Wopambanazonse,
Iye amene
amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Adzanena kwa
Chauta kuti, “Inu ndinu kothawira kwanga,
ndi linga
langa, Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Mukhale nane,
Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Zoipa sizidzakugwera,
Zoopsa
sizidzafika pafupi ndi nyumba yako,
Chauta
adzapatsa angelo ake,
Ntchito yoti
azikulonda kulikonse kumene upite.
Mukhale nane,
Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Adzakunyamula
m' manja mwao,
kuwopa kuti
phazi lako lingapweteke ndi mwala,
Udzatha kuponda
mkango ndi njoka,
Zoonadi
udzaponda ndi phazi lako,
Msona wa mkango
ndiponso chinjoka.
Mukhale nane,
Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Pakuti amene
amandikangamira, Ine Mulungu,
Mwachikondi,
ndidzampulumutsa.
Ndidzamteteza
popeza kuti amadziwa dzina langa.
Akadzandiitana,
ndidzamuyankha,
Ndidzakhala
naye pa nthawi yamavuto,
Ndidzamlanditsa
ndi kumlemekeza.
Mukhale nane,
Ambuye, pa nthawi yamavuto.
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA:
MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 10: 08 – 13.
(Zikhulupiriro za Akhristu.)
Abale, Malembo
akuti chiyani? Akuti, ‘Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima
mwako.’ Amenewa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timawalalika. Ngati uvomereza
ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti
Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu amati
akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo
amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka. Paja Malembo
akuti, ‘Munthu aliyense wokhulupirira lye, sadzachita manyazi.’ Choncho palibe
kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a
onse, ndipo amadalitsa moolowa manja onse otama dzina lake mopemba. Ndi monga momwe
mau a Mulungu anenera kuti, ‘Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba
adzapulumuka.’
Mau a
Ambuye.................................Tithokoze Mulungu.
NYIMBO
YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04: 04b.
Ulemerero ndi
mayamiko kwa Inu, Khristu.
Munthu
sangakhale moyo ndi chakudya chokha,
koma ndi mau
onse olankhula Mulungu.
Ulemerero ndi
mayamiko kwa Inu, Khristu.
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA
WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 04: 01 – 13. (Mzimu Woyera yo
ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana
ankamuyesa.)
Yesu, ali
wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu
Woyerayo ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana
ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha,
adamva njala. Tsono Satana adamuuza kuti, “ngati ndinu Mwana wa Mulungu,
lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.” Koma Yesu adati. “Malembo
akuti, ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha.’ Pambuyo pake Satana
adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang'ono adamuwonetsa
maiko a mafumu onse a pansi pano. Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani
ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo
ndimazipatsa aliyense amene ndifuna. Choncho mukandipembedza, zonsezi
zidzakhala zanu.” Apo Yesu adati, “Malembo akuti, Uzipembedza Ambuye Mulungu
wako, ndipo uziwatumikira Iwo okha.” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye
ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza
kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti,
Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni ndiponso, Iwo adzakunyamulani
m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.” Koma Yesu adati, “Malembo
akuti, Usawayese Ambuye, Mulungu wako.” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa
zonsezi, adalekana naye, kudikira nthawi ina.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye
Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment