Saturday, February 26, 2022

LAMULUNGU LA 08 PA CHAKA C

(‘Munthu wabwino amazindikirika chifukwa cha zochita zake.’)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPHUNZITSI: MPHUNZITSI 27: 04 – 07. (Usatamande munthu usanamve zolankhula zake.)

Munthu akagwedeza sefa, zinyatsi zimatsalira momwemo. Chimodzimodzinso zolakwa za munthu zimaoneka iye akamalankhula. Monga mbiya amaiyesa pa moto, momwemonso munthu amayesedwa pa zokamba zake. Monga chipatso cha mtengo chimatidziwitsa luso la mlimi, momwemonso zokamba za munthu zimaonetsa zimene zili mumtima mwake. Usatamande munthu usanamve zolankhula zake, poti mayeso enieni a anthu ali pamenepa.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

Nkwabwino kuthokoza Chauta,

Kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.

Nkwabwino m'mawa kulalika za chikondi chanu chosasinthika,

Ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu.

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta,

Yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba,

Nthawi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriwira,

Imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama.

iye ndiye thanthwe langa, mwa Iye mulibe chokhota.

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

----------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 15: 54 – 58 (Tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.)

Abale, thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, Imfa yagonjetsedwa kwathunthu. Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti? Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziwa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: AFILIPI 02: 15d,16a.

Alleluia, Alleluia – Pakati pa anthu mumawala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi pakuwauza mau opatsa moyo. – Alleluia, Alleluia.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 06: 39 – 45. (Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.)

Yesu adawapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse awiri sadzagwa m'dzenje kodi? Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake. Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m' maso mwakoka, pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m’maso mwa mbale wako. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapenanso mtengo woipa kubala zipatso zabwino. Mtengo uliwonse umadziwika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, February 19, 2022

LAMULUNGU LA 07 PA CHAKA C

(Kondani adani anu, muwachitire zabwino.)

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 01 SAMUELE 26: 02. 07 – 09.12 – 13, 22 – 23. (Chauta anakuperekani m' manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.)

Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko. Choncho Davide ndi Abisai adakalowa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira. Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kawiri.” Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?” Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziwa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaawagonetsa tulo tofa nato. Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu. Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge. Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m' manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.

Mawu a Ambuye....................................................................................................…Tithokoze Mulungu.

----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 08, 10, 12 – 13.

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera,

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.


Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,

Ndi kuchiritsa matenda ako onse,

Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda,

Amakuveka chikondi ndiponso chifundo chake, ngati chisoti chaufumu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga,

Ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu,

Satilanga moyenerera machimo athu,

Satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe,

Ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu,

Monga bambo amachitira chifundo ana ake,

Ndi momwenso Chauta amawachitira chifundo omulemekeza.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15:45 – 49. (Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba.)

Abale, Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo. Loyamba sithupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu. Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano, Koma Khristu, Adamu wachiwiri uja, anali wochokera Kumwamba. Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba. Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa kumwamba.

Mawu a Ambuye….................................................................................................Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------------------------NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: YOHANE 13:34.

Alleluia, Alleluia – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana; monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana, atero Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

-------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 06: 27 – 38 (Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.)

Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziwachitira zabwino amene amadana nanu. Muziwafunira madalitso amene amakutembererani, muziwapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze. Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amawakonda. Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi. Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziwa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe. Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo. Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mthenga wa Ambuye….....................................................Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/


 

Saturday, February 12, 2022


 LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA C
(Kodi munthu wodala ndani?)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 17: 05 – 08. (Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake; ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta.)

Chauta akunena kuti, “tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake, amene amagonera pa munthu mnzake kuti amthandize, pamene mtima wake wafulatira Chauta. Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo. Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwamadzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhawa, ndipo suleka kubala zipatso.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 01: 01 – 04.06

 

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.

 

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa,

Wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa,

Wosakhala nawo m’gulu la anthu onyoza Mulungu,

Koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta,

Nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

 

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.

 

Munthuyo ali ngati mtengo

Wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi.

Ngati mtengo wobereka zipatso pa nthawi yake,

Umene masamba ake safota konse.

Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

 

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.

 

Anthu oipa sali choncho,

Ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo.

Paja Chauta amawasamalira anthu ake.

koma anthu ochimwa adzaonongeka.

 

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.

------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15: 12, 16 – 21. (Ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake.)

Abale, popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso”? Pakuti ngati akufa sauka, Khristunso sadauke. Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu. Pamenepo nawonso amene adamwalira ali okhulupirira Khristu, adatayika ndithu. Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse. Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka.

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: LUKE 06: 23ab.

Alleluia, Alleluia – Sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba – Alleluia, Alleluia.

-------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 06: 17, 20 – 26. (Ndinu odala, inu osaukanu. Koma ndinu atsoka, anthu achumanu.)

Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi kumbali yakunyanja, ku Tiro, ndi Sidoni. Yesu adayang’ana ophunzira ake, nawauza kuti, “Ndinu odala, inu Osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu. Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa. Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. Nthawi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankawachita aneneri kale. Koma ndinu atsoka, anthu achumanu, chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani. Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu, chifukwa mudzamva njala. Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu, chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira. Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Sunday, February 6, 2022

 LAMULUNGU LA 05 PA CHAKA C

(Ambuye! Ndilipo, munditume.)

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YESAYA: YESAYA 06: 01 – 08. (Ndilipo ineyo, tumeni.)

 

Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri ophimbira kumaso, awiri ophimbira mapazi, awiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi. Chifukwa cha kufuulako maziko onse ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m’Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha. Apo ine ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse.” Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja adaulukira kwa ine, ali ndi khala lamoto m’manja mwake. Khalalo adalichotsa pa guwa la nsembe ndi mbaniro. Ndipo adandikhuza pakamwa ndi khala lamotolo nati, “taona, ndakukhudza milomo ndi khalali. Kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.” Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati, “ndilipo ineyo, tumeni.”

 

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------------------

 

 NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138: 01 – 05, 07 – 08.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

 

Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse,

Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu,

Ndikugwada mowerama,

Kunyumba kwa Nyumba yanu yoyera.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

 

Ndikutamanda dzina lanu,

Chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,

Chifukwanso cha kukhulupirika kwanu,

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha,

Mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

 

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

 

Mafumu onse a m’dziko adzakutamandani, Inu Chauta,

Chifukwa amva mau a pakamwa panu,

Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta,

Pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

 

Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya,

Dzanja lanu lamanja limandipulumutsa,

Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya,

Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta.

------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15: 01 – 11. (Zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso.)

 

Abale, ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira, ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba. Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe. Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera. Motero adaonekera Kefa, kenaka atumwi khumi ndi awiri aja. Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthawi imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira. Ndipo adaonekera Yakobo, kenaka atumwi onse. Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo, ngakhale ndili ngati mpolo chabe. Inetu ndine wamng'onong'onodi mwa atumwi onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza Mpingo wa Mulungu. Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa. Motero kaya ndi ineyo kaya ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso.

 

Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.

-----------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO: MATEYO 04: 19.

 

Alleluia, Alleluia – Inu, munditsate, atero Ambuye, ndikakusandetseni asodzi a anthu – Alleluia, Alleluia.

-------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 05: 01 – 11. (Adasiya zonse namatsata Yesu.)

 

Tsiku lina Yesu adamirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete, anthu ambirimbiri nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu. Iye adaona zombo ziwiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao. Yesu adalowa m'chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuwaphunzitsa anthuwo. Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, "Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba." Simoni adati, "Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka." Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika. Adachita kukodola anzao a m'chombo china chija kuti adzawathandize. Iwo adabwera, ndipo adadzaza zombo ziwiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira. Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuwerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, "Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa." Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo. Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni, nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, "Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu." Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: Mkatolikamw

 

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...