LAMULUNGU LA 07 PA
CHAKA C
(Kondani adani
anu, muwachitire zabwino.)
Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko. Choncho Davide ndi Abisai adakalowa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira. Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kawiri.” Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?” Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziwa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaawagonetsa tulo tofa nato. Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu. Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge. Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m' manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.
Mawu a Ambuye....................................................................................................…Tithokoze Mulungu.
-----------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 08, 10, 12 – 13.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Moyo wanga wonse
umuyamike potchula dzina lake loyera,
Tamanda Chauta,
iwe mtima wanga,
Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Ndiye amene
amakhululukira machimo ako onse,
Ndi kuchiritsa
matenda ako onse,
Ndiye amene
amapulumutsa moyo wako ku manda,
Amakuveka chikondi
ndiponso chifundo chake, ngati chisoti chaufumu.
Chauta ndi
wachifundo ndi wokoma mtima.
Chauta ndi
wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga,
Ndipo chikondi
chake chosasinthika nchachikulu,
Satilanga
moyenerera machimo athu,
Satibwezera
molingana ndi zolakwa zathu.
Chauta ndi
wachifundo ndi wokoma mtima.
Monga kuvuma kuli
kutali ndi kuzambwe,
Ndi momwenso
amachotsera zolakwa zathu,
Monga bambo
amachitira chifundo ana ake,
Ndi momwenso
Chauta amawachitira chifundo omulemekeza.
Chauta ndi
wachifundo ndi wokoma mtima.
------------------------------------------------------------------------------------------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15:45 – 49. (Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba.)
Abale, Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo. Loyamba sithupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu. Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano, Koma Khristu, Adamu wachiwiri uja, anali wochokera Kumwamba. Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba. Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa kumwamba.
-----------------------------
Alleluia, Alleluia – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana; monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana, atero Ambuye. – Alleluia, Alleluia.
-------------------------------
Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziwachitira zabwino amene amadana nanu. Muziwafunira madalitso amene amakutembererani, muziwapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze. Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amawakonda. Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi. Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziwa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe. Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo. Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Mthenga wa Ambuye….....................................................Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment