Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C
“Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (CHIYAMBI); GENESIS 14:18-20. (Adatenga buledi ndi vinyo).
Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga Buledi ndi Vinyo. Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu. Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zimene adaalandira.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 110:1-4.
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja,
mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta adzakuza ufumu wako wamphamvu kuchokera ku Ziyoni.
Adzati, “Khala mfumu yolamulira adani ako.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Anthu ako adzadzipereka mwaufulu pa tsiku limene udzaonetse mphamvu zako pa phiri loyera.
Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu unyinji wao, monga m’mene mame amabwerera m’mamawa.
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake akuti,
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 1 AKORINTO 11:23-26. (Nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye).
Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.’’ Momwenso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthawi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.’’ Pakuti nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—Yohane 6:51.
Alleluia, Alleluia!! – Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia!!
--------------------------------------
NYIMBO YA UKARISTIA (SEQUENCE)
O SIYONI UYAMIKE
Mbusa wabwino, Buledi weniweni,
Mbuye Yesu, mutichitire chisoni.
Muteteze, nkulowetsa
Nkhosa zanufe kumwamba.
1. O Siyoni, uyamike
Mpulumutsi wako, Mbuye,
Mfumu ndinso Mbusa wako.
2. Sudzafika kuimbira
Mlungu wako mokwanira.
Ukwezetu mawu ako.
3. Nkofunika ndithu lero
Kutama Buledi wamoyo,
Ngwopatsa moyo womwewo.
4.Tidziwa mosapeneka
Kuti Yesu anapatsa
Bulediyu kwa apositoli.
5. Tsono tisankhule nyimbo
Zokoma kwambiri lero
Ndi kuimba mwachimwemwe.
6. Misa itibweretsera
Tsiku lomwe la kupanga
Phwando loyerayerali.
7. Ndi Pasaka yatsopano
Ya Mfumu yatsopanonso
Miyambo yakale yatha.
8. Zalero zibadiritsa
Zakale, monga kuyera
M'mawa kuchotsatu mdima.
9. Yesu anatilamula
Kubwereza zomwe zija
Anazichita tsikuli.
10. Pomvera Yesu ifenso
Tisandutsa buledi n'vinyo
Pa nsembe yopulumutsa.
11. Buledi asanduka Thupi
Ndiponso vinyo Magazi
A Khristu, Ambuye athu.
12. Sitimvetsa, sitiona,
Koma ndithu tizimvera
Zozizwitsa zimenezi.
13. Buledi ndinso vinyo ali
Chizindikiro chophimba
Zazikulu zobisika.
14. Tidya Thupi la Ambuye
Ndi kumwa Magazi ake:
Akhala muziwirizi.
15. Aliyense amlandira
Wathunthudi, wosasweka,
Ndi wosagawika konse.
16. Nayo Buledi wa anjelo
Ngwa alendofe tsopano
Manna wotipatsa nyonga.
17. Mulungu wamphamvuzonse
Ndiponso wodziwa zonse,
Inu mutidyetsa pano.
18. Mutidyetsenso Kumwamba
M'phwando la anthu oyera.
Amen. Amen. Aleluya.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 9:11b-17. (Anthu onse aja adadya nakhuta).
Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adawalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuwa lili pafupi kulowa, ophunzira khumi ndi awiri aja adadzauza Yesu kuti, “bwanji anthuwa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.’’ Koma Yesu adawauza kuti, “inuyo apatseni chakudya.’’ Iwo adati, “tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziwiri zokha. Kaya kapena tipite tikawagulire anthu onsewa chakudya?’’ Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “auzeni anthuwa akhale pansi m’magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.’’ Ophunzira aja adawakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziwiri zija, nayang’ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi awiri.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti nsembe ya Ukaristia ndi gwero la zabwino za chipulumutso, tigwirizane naye Yesu Khristu wansembe wathu wamuyaya, popereka mapemphero athu kwa Mulungu Atate:
1. Tipempherere akhristu onse kuti apeze m’sakramenti la Ukaristia mphamvu zoyeretsa moyo wao wa tsiku ndi tsiku, pakuphathana kwenikweni ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere anthu onse amene akusauka ndi njala, matenda ndi umphawi, kuti apeze chithandizo chochokera kwa anzawo achikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anyamata amene Mulungu akuwaitana ku unsembe kuti avomere kuitanidwa kwao ndipo alimbikire pa maphunziro ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tipemphererane ife tonse a m’parishi yathu ino, kuti tikhale amodzi ndi kumakondana mwaubale, pakulandira Ukaristia kawirikawiri.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani, chifukwa potiitana ku phwando loyerali, mwatipatsa mwai wa kulumikizana tonse m’chikondi chanu. Mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB