Saturday, June 28, 2025

Chaka cha Petro ndi Paulo Oyera, Apostoli.

Chaka cha Petro ndi Paulo Oyera, Apostoli.

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 12:1-11.

 

Tsopano ndikudziwadi kuti Ambuye andipulumutsa kwa Herode. Pafupi ngati nthawi imeneyo mfumu Herode adagwira ena a mu Mpingo kuti awazunze. Adalamula kuti Yakobo, m’bale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Pasaka, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Atamgwira, adamtsekera m’ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Pasaka chitapita. Motero Petro ankasungidwa m’ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza. Usiku woti m’mawa mwake Herode azenga mlandu wake, Petro adaagona pakati pa asilikali awiri. Anali womangidwa ndi maunyolo awiri, ndipo pakhomo pa ndende panali alonda ena. Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuwala koti mbee kudaunika m’chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m’nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m’manja mwake. Kenaka mngelo uja adamuuza kuti, “Vala lamba wako ndi nsapato zako.” Petro atachita zimenezi mngelo uja adamuuzanso kuti, “Fundira mwinjiro wako, unditsate.” Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m’masomphenya chabe. Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiwiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata cholowera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera. Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziwadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34:1-8.

 

Mnjelo wa Ambuye amapulumutsa iwo amene amamvera Mulungu.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza.

Moyo wanga umanyadira Chauta.

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Mnjelo wa Ambuye amapulumutsa iwo amene amamvera Mulungu.

 

Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta,

Tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.

Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha.

Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.

 

Mnjelo wa Ambuye amapulumutsa iwo amene amamvera Mulungu.

 

Ozunzikawo atayang’ana kwa Chauta,

Nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi.

Munthu wosauka adalira. ndipo Chauta adamumva,

Nampulumutsa m’mavuto ake onse.

 

Mnjelo wa Ambuye amapulumutsa iwo amene amamvera Mulungu.

 

Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye,

Ndipo amawapulumutsa.

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

Ngwodala munthu wothawira kwa Chauta.

 

Mnjelo wa Ambuye amapulumutsa iwo amene amamvera Mulungu.

 

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 2 TIMOTEO 4:6-8. 17-18.

 

Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo. Wokondeka wanga, ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m’moyo uno. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso. Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse awamve. Motero ndidapulumuka m’kamwa mwa mkango. Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundilowetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—
MATEYO 16:18.

Alleluia, Alleluia!! – “Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.” – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 16:13-19 (Ndiwe Petro, ndipo ndidzakupatsa makii a Ufumu wakumwamba).

 

Pamene Yesu adafika ku madera a ku Kesareya-Filipi, adafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthune ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.” Apo Yesu adawafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba. Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. Ndidzakupatsa makii a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A [Gaudete Sunday] “Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”   MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’N...