LAMULUNGU LA 5 MU NYENGO YA LENTI – C
“Pita, usakachimwenso.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 43: 16 – 21 (Ndikuchita zinthu zatsopano ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa).
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiwatiwa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.”
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 126:1-6.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,
Tinali ngati anthu amene akulota.
Pamenepo tidasekera kwambiri,
Ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti,
Chauta wawachitira zazikulu.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,
ndipo tasangalala.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,
tikhale ngati mtsinje yam'chipululu.
Anthu amene amafesa akulira,
Adzakolola akufuula ndi chimwemwe.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Munthu amene amapita akulira,
Atatenga mbeu zokafesa, adabwerera kwao
Akufuula ndi chimwemwe,
Atatenga mitolo yake yambiri.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 3:8-14 (Ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu).
Abale, zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu, Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira. Chimene ndikufuna nchakuti ndidziwe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zowawa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi pokhulupirira kuti inenso ndidzakhala ndi moyo wosatha podzauka kwa akufa. Za kuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liwiro. Sindikunena kuti ndafikapo kale pa zimenezi, kapena kuti ndine wangwiro kale. Koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuzipata pakuti ndicho chinali cholinga cha Yesu Khristu pakundikopa kuti ndikhale wake. Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiwala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto ampikisano wa liwirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOWELE 2:12-13.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu – Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 8:1-11. (Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala).
Yesu adapita ku Phiri la Olivi. M'mamawa adabweranso ku Nyumba ya Mulungu. Anthu onse adadza kwa lye, Iyeyo nkukhala pansi nayamba kuwaphunzitsa. Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. Paja M'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?’ Adaamufunsa funsoli kuti amuyese ndi kumpeza chifukwa. Koma Yesu adawerama, nayamba kulemba pansi ndi chala chake. Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaweramuka nawauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.” Atatero, adaweramanso namalemba pansi. Koma iwo atamva zimenezi, adayamba kuchokapo m’modzim’modzi, kuyambira akuluakulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pompaja. Kenaka Yesu adaweramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi m’modzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mulungu safuna kuti wochimwa afe, koma alape ndi kukhala moyo. Tiyeni tsono, tonse tigwirizane popereka mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu anzathu amene adaleka kupemphera adzidzimuke mumtima mwao ndi kubwerera kwa Mulungu, pokumbukira imfa ya Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akulu oweruza milandu asenze udindo wao mokhulupirika ndi mofatsa aziwonetsa mtima wachifundo poweruza anthu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipempherere ife tomwe kuti tileke kuganizira anzathu zoipa, koma tidziwe kuwalangiza mofatsa ndi mowamvera chifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate okoma mtima, musaleke kutigwira dzanja ndi kutidzutsa ife ana anu ofooka, kuti tiyende pamaso panu molimbika ndi mosangalala. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
No comments:
Post a Comment