Saturday, October 25, 2025

LAMULUNGU LA 30 PACHAKA—C.

LAMULUNGU LA 30 PACHAKA—C.

“Mundichitire chifundo wochimwane!”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA SIRAKI (MPHUNZITSI): SIRAKI 35: 12-14, 16-19. (Pemphero la munthu wodzichepetsa limabzola mitambo).

 

Usayese kupereka chiphuphu kwa Ambuye, chifukwa sadzachilandira. Ndipo usadalire nsembe yopanda chilungamo, chifukwa Ambuye ndiwo muweruzi, muweruzi wake wopanda tsankho. Saonetsa kukondera poweruza wosauka, amamvera pemphero la amene anzake adamulakwira. Sanyozera pempho la mwana wamasiye kapena madandaulo a mkazi wamasiye. Uzitumikira Ambuye mokhulupirika, ndipo iwowo adzakulandira. Pamenepo mapemphero ako akafika kumwamba. Pemphero la munthu wodzichepetsa limabzola mitambo, ndipo mtima wake sudzakhazikika mpaka Ambuye atamva pempherolo. Sadzaleka kupempha mpaka wopambanazonse atamuyendera, ndi kuchitira chilungamo anthu abwino pakuweruza moona. Ambuye sadzachedwa ndipo sadzapirira anthu ochimwa, mpaka atadzaphwanya misana ya anthu opanda chisoni, ndi kulipsira mitundu ya akunja; mpaka ataonongeratu anthu achipongwe ndi kuthyola mphamvu za anthu osalungama; mpaka aliyense atampatsa molingana ndi zochita zake, ndi kulipira ntchito zakezo potsata zolinga za mumtima mwake; mpaka atagamula mlandu wa anthu ake, ndi kuwasangalatsa ndi chifundo chao. Panthawi ya mavuto chifundo cha Ambuye nchokondweretsa, ngati mitambo yamvula panthawi ya chilala.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34:2-3, 17-19, 23.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza,

Moyo wanga umanyadira Chauta,

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Koma Chauta amawakwiyira anthu ochita zoipa,

Anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano,

Pamene anthu ake akulira kuti awathandize,

Chauta amamva nawapulumutsa m’mavuto ao onse.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka,

Amapulumutsa otaya mtima,

Chauta amaombola moyo wa atumiki ake,

Palibe wothawira kwa Iye amene adzalangidwe.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 2 TIMOTEO 4:6-8, 16-18. (Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira).

 

Paja ine ndiye moyo wanga Wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m’moyo uno. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro, ndasunga chikhulupiliro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungura. Ambuye amene ali woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphotoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso. Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandizira, onse adangondisiya ndekha. Mulungu awakhululukire. Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a uthenga wabwino, kuti anthu amitundu yonse awamve. Motero ndidapulumuka m’kamwa mwa mkango. Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundilowetsa mu ufumu wake kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO— 2 AKORINTO 5:19.

Alleluia, Alleluia!!—Mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiwalalike. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 18: 9-14. (Wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai).

 

Yesu adawapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzawo. Adati, “Anthu awiri adapita ku nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. Ine ndimasala zakudya kawiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang’ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’” Yesu popitiriza mau adati, “kunena zoona, wokhometsa mnsokhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, ngakhale ndife anthu ochimwa, tisaope kukweza mapemphero athu kwa Atate a Kumwamba, popeza kuti iwo amamvera chifundo anthu odzichepetsa:

 

1.     Tipempherere ansembe ndi atsogoleri a Mpingo, kuti atumikire akhristu ao mwachifundo ndi modzichepetsa, podziwa kuti iwonso alikusowa chikhulupiriro.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Tipempherere akhristu akugwa ndi onse amene adaleka kupemphera kuti adzidzimuke ndi kutembenukira kwa Mulungu, pozindikira kuti Iye ndiyedi Atate achifundo.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Tipempherere mabanja achikhristu, kuti eni ake alimbikire kupemphera m’nyumba mwao masiku onse, ndipo ana ao aphunzirepo nzeru zokhulupirira Mulungu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Tidzipempherere ife tomwe, kuti tilekeretu kuganizira anzathu zoipa. Tizithandizana mwaubale, modzichepetsa mtima pokumbukira kuti aliyense ali ndi zoperewera zake.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mutichitire chifundo ife ana anu ochimwa. Mutichotsere maganizo akunyada ndi akudzikhulupirira, kuti tiyende molunjika m’njira ya malamulo anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, October 18, 2025

LAMULUNGU LA 29 PACHAKA—C.

LAMULUNGU LA 29 PACHAKA—C.

“Mulungu adzatithandiza tikamapempha ndi mtima woona.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO: EKISODO 17:8-13. (Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo).

 

Tsono kudabwera Aamaleke ku Redifidimu kudzamenyana ndi Aisraele. Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, mawa mupite kukamenya nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.” Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthawi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri. Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana. Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Awiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwira manja a Mose aja. Adawagwirira ndithu mpaka dzuwa kulowa. Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 121:1-8.

 

Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

 

Ndimakweza maso anga ku mapiri,

Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?

Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta,

Amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

 

Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

 

Sadzalola phazi lako literereke,

Iye amene amakusunga sadzaodzera,

Zoonadi, amene amasunga Israele,

Ndithu sadzaodzera kapena kugona.

 

Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

 

Chauta ndiye amene amakusunga,

Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja,

Dzuwa silidzakupweteka masana,

Mwezi sudzakuvuta usiku.

 

Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

 

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse,

Adzasamala moyo wako,

Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita,

Kuyambira tsopano mpaka muyaya.

 

Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 2 TIMOTEO 3:14—4:2. (Munthu amene ndi wa Mulungu amakhala wokonzeka kugwira ntchito ina iliyonse).

 

Wokondeka Timoteo, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziwa kuti nzoona, paja ukuwadziwa amene adakuphunzitsa. Ukudziwanso kuti kuyambira ukali mwana wawazolowera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupilira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adawalembetsa mochita ngati kuwauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita Ntchito yabwino iliyonse. Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndiufumu wake wa Khristuyo. Ndikukulamula ndithu kuti uzilalikira mau a Mulungu. Uziwalalika molimbikira, pa nthawi imene anthu akuwafuna. Uziwalozera zolakwa zao, uziwadzudzula, uziwalimbitsa mtima, osalephera kuwaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO— AHEBRI 4:12.

Alleluia, Alleluia!!—Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 18:1-8. (Nanga Mulungu, angaleke kuwaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku?).

 

Yesu adawaphera Fanizo pofuna kuwaphunzitsa kuti azipemphera nthawi zonse, osataya mtima. Adati, “m’mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. M’mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzapempha kuti, ‘mundiweruzireko mlandu wanga umene uli pakati ine ndi mdani wanga.’ Kwa nthawi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘ngakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu, komabe chifukwa cha mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’” Tsono Ambuye adati, “mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. Nanga Mulungu, angaleke kuwaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangowalekerera? Iyayi, kunena zoona adzawaweruzira mlandu wao mnsanga. Komabe mwana wa munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, pakuti Yesu Khristu akutitsogolera m’mapemphero athu, tiyeni tipereke ulemu kwa Atate a Kumwamba popempherera anthu onse:

 

1.     Tipempherere Apapa, Aepiskopi, ndi ansembe onse, kuti alondoloze akhristu ao m’njira ya kupemphera, pakulimbitsa chikhulupiriro m’mitima mwao.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     ⁠Tipempherere anthu onse amene sapemphera, kuti azindikire umphawi wao ndi kumatembenukira kwa Mulungu, pokhulupirira chifundo chake chofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     ⁠Tipempherere mabanja achikhristu, kuti eni ake alimbikire kupemphera masiku onse, pamodzi ndi ana ao, ndipo motero akhazikike m’chikondi cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tipempherere anthu a m’zipani odzipereka ku moyo wobindikira, kuti mapemphero ao ndi zitsanzo zao zidzetse mtendere ndi madalitso kwa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     ⁠Tipemphererane ife tomwe kuti timange moyo wathu pa chikondi cha Mbuye pokhala anthu okonda kupemphera nthawi zonse: ndipo motero tibale zipatso zokhalitsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tilikuyamika chikondi chanu chosasinthika ndi chifundo chanu chopanda malire. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, October 11, 2025

LAMULUNGU LA 28 PACHAKA—C

LAMULUNGU LA 28 PACHAKA—C

“Tithokoze Ambuye, Mulungu wathu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU: 2 MAFUMU 5:14-17. (Naamani adabwerera kwa Elisa ndipo anamvera Mulungu wa ku Israele).

 

Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m’madzimo kasanunkawiri, malinga ndi m’mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa. Pambuyo pake Naamani pamodzi ndi onse omperekeza, adabwerera kwa mneneri wa Mulungu uja. Adadzaima pamaso pa Elisa namuuza kuti, “ndithu, ine ndadziwa tsopano kuti padziko lonse lapansi kulibe Mulungu wina, koma wa ku Israele yekha. Tsono landirani mphatsoyi kwa ine mtumiki wanu.” Koma Elisa adati, “pali Chauta, Mulungu wamoyo, amene ndimamtumikira, ine sindilandira zimenezi.” Naamani adamkakamiza kuti atenge, koma iye adakana ndithu. Tsono Naamani adati, “ngati mukukana, ine ndikukupemphani kuti mundilole ine mtumiki wanu nditengeko dothi lokwanira kunyamula abulu awiri. Pakuti kuyambira tsopano ine sindidzaperekanso nsembe zopsereza, kapena nsembe ina iliyonse, kwa mulungu wina aliyense, koma kwa Chauta basi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98:1-4.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono,

Wake woyera zampambanitsa.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Chauta waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse,

Kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,

Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulirani Chauta ndi Chimwemwe, inu dziko lonse lapansi,

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 2 TIMOTEO 2:8-13. (Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye).

 

Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali m’modzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika. Chifukwa cha uthenga wabwinowu ndimamva zowawa, mpakanso kumangidwa m’ndende, ngati chigawenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa. Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adawasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya. Awa ndi mau otsimikiza ndithu: ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye. Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, iyenso adzatikana. Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupilika, pakuti sangathe kudzitsutsa.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO— 1 ATESALONIKA 5:18.

Alleluia, Alleluia!!—Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 17:11-19. (Sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu).

 

Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu adadzera m’malire a Samariya ndi Galileya. Pamene ankalowa m’mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali, nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.” Pamene Yesu adawaona, adawauza kuti, “pitani, kadziwonetseni kwa ansembe,” Pamene iwo ankapita, adachira. Tsono m’modzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau. Adagwada nkuwerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo adali Msamariya. Apo Yesu adati, “kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti? Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?” Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, pokumbukira zabwino zonse zimene Mulungu adatichitira, tiyeni tiyamike Atate athu a kumwamba. Ndipo tiwapemphe kuti apitirize kutsira madalitso ao pa ife ndi pa anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti adziwe kuyamika Mulungu masiku onse, pozindikira kuti Ambuye alikuwatsogolera ku Ufumu wa Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Tipempherere anthu a mafuko onse amene sanamvebe Mthenga Wabwino, kuti nawonso azindikire kukoma mtima kwa Mulungu ndipo adziwe kumthokoza.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Tipempherere anthu akhate, odwala ena onse a m’dziko lapansi, kuti alandire chisamaliro chokwanira ndiponso chikondi chowathandiza kupirira mavuto ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     ⁠Tidzipempherere ife amene tili muno, kuti tikhale nawo mtima wodziwa kuthokoza Mulungu nthawi zonse, ngakhale pamene tili m’mavuto.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, ife tonse ana anu tikukuyamikani kuti ndinu wokoma mtima kopambana, ndipo tidzatamanda chifundo chanu nthawi zonse ndi pamalo ponse, m’dzina la Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, October 4, 2025

LAMULUNGU LA 27 PACHAKA—C

LAMULUNGU LA 27 PACHAKA—C

“Ambuye, mutiwonjezere chikhulupiliro.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI HABAKUKU: HABAKUKU 1:2-3; 2:2-4. (Ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake).

 

Kodi inu Chauta, ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo nthawi yaitali bwanji, inuyo osandiyankha? Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,” Inuyo osatipulumutsa? Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto oterewa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri. Chauta adandiyankha kuti, “lemba uthengawu, ulembe mooneka bwino pa mapale, kuti wowerenga awerenge mosavuta. Uthengawu ukudikira nthawi yake. Nthawi yakeyo idzabwera mofulumira, sizidzalephera kuchitika. Ngati ziwoneka kuti zikuchedwa, mudikire. Zidzafika ndithu, si kuchedwa ai. Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.

 

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95:1-2, 6-9.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Bwerani, timuimbire Chauta,

Tiyeni tifuule ndi Chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa,

Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,

Timuimbire nyimbo zotamanda.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Bwerani, timpembedze ndi kumlambira,

Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,

Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,

Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Lero mukadamverako mau ake!

Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,

Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,

Pamene makolo anu anandiputa mondiyesa,

Ngakhale anali ataona ntchito zanga.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 2 TIMOTEO 1:6-8, 13-14. (Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu).

 

Wokondeka, nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto. Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira. Usachite manyazi tsono kuchita umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m’ndende chifukwa cha Iye, koma umve nao zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu ya Mulungu. Uwagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti udzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

 

Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO— 1 PETRO 1:25.

 

Alleluia, Alleluia!!—Mau a Mulungu ngokhala mpaka muyaya. Mau amenewa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU:  MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 17:5-10. (Mutiwonjezere chikhulupiriro).

 

Atumwi adapempha Ambuye kuti, “mutiwonjezere chikhulupiriro.” Koma Yesu adati, “mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambewu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘zuka, kadzibzale m’nyanja.’ Ndipo ukadakumveranidi ndithu.” Yesu adatinso, “utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woweta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘bwera mnsanga, udzadye?’ Sungatero ayi, koma udzamuuza kuti, ‘konzere chakudya. Ukonzeke kunditumikira mpaka ineyo ndidye ndi kumwa. Iweyo udya ndikumwa ndi kudya pambuyo pake. Kodi ungamuthokoze wantchitoyo chifukwa chakuti wachita zimene unamlamula? Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti, ‘Ndife antchito osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, patokha sitingathe kuchita kanthu kotiyeneretsa kukafika ku Ufumu wa Kumwamba. Tsono tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atiwonjezere chikhulupiriro:

 

1.     ⁠Tipempherere akulu osenza maudindo osiyanasiyana mu Mpingo, kuti apitirize ntchito yao yolalika Mthenga wa Yesu mokhulupirika ndi modzichepetsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu amene akuzunzidwa chifukwa cha Mthenga Wabwino, kuti aonetse chikhulupiriro cholimba, pomapirira mavuto mosataya mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     ⁠Tipempherere akhristu amene adafooka pa chikhulupiriro chao, kuti aikolere mphatso imeneyo pakupemphera mwakhama, mpaka kuti iyakenso ngati moto.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     ⁠Tipempherere ife tonse amene tasonkhana muno, kuti mau athu ndi mayendedwe athu atsimikizire anthu onse kuti taikadi chikhulupiriro chathu chonse pa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate okoma mtima, musaleke kutiwongolera ndi Mzimu Woyera, kuti tiyende molimbika m’njira ya chipulumutso pakutumikira Inu ndi anzathu ndi mtima wachikondi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

 

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A [Gaudete Sunday] “Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”   MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’N...