Saturday, December 13, 2025

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

[Gaudete Sunday]

“Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA: YESAYA 35:1-6a, 10. (Mulungu Mwini akubwera kudzakupulumutsani).

 

Chipululu ndi dziko lopanda madzi ndidzasangalala, dziko luoma lidzakondwa ndi kuchita maluwa. Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu. Mulimbitse manja ofooka, ndi kuwapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.” Pamenepo maso a anthu akhungu adzapenyuka, ndipo makutu a agonthi adzatsekuka. Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m’chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m’dziko louma. Amene Chauta adawaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi Chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146:6-10.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amasunga malonjezo ake nthawi zonse,

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,

Amawapatsa chakudya anthu anjala,

Chauta amamasula am’ndende.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,

Chauta amakweza anthu otsitsidwa,

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Chauta amateteza alendo, Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Koma njira za anthu oipa amazipotoza,

Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,

Mulungu wako, iwe Ziyoni, dzalamulira ku mibadwo yonse,

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA YAKOBE: YAKOBE 5:7-10. (Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera).

 

Abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m’mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m’munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokolansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera. Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m’dzina la Ambuye. Iwo adamva zowawa, komabe adapirira.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—YESAYA 61:1 (LUKA 4:18)

Alleluia, Alleluia!!—Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa Ine. Wandituma kuti ndikalalike uthenga Wabwino kwa anthu osauka. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 11:2-11. (Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?)

 

Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukafunsa kuti, “kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona. Akhungu akupenya ndipo Opunduka miyendo akuyenda; akhathe akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphawi akumva uthenga wabwino. Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha ine.” Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “kodi m’mene mudaapita ku Chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Iyai, anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za mafumu. Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, ‘nayitu Nthumwi yanga, ndikuituma m’tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamn’gonong’ono mu ufumu wakumwamba amampambana.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pokhala tikudziwa kukoma mtima kwa Mulungu Atate athu, tiyeni timupemphe kuti alimbitse chikhulupiriro mwa anthu onse:

 

1.     Akhristu onse aonetse ndi mau ao ndi ntchito zao kuti Ambuye adabweradi pansi pano, ndipo kuti alikupitiriza ntchito yao yotipulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu akhungu, agonthi, olumala ndi odwala onse alimbe mtima. Pozindikira kuti Yesu Khristu adadzera iwowo, nawaonetsa chifundo chopambana.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atsogoleri a mpingo apitirize ntchito yao mwakhama ndi mopirira mpaka Ambuye adzabwerenso.
Tikupemphani mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno, mau athu ndi machitidwe athu adzetse chikhulupiriro ndi chimwemwe m’mitima ya anzathu pa masiku ano odikira Khrismasi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa, ndipo mutiphunzitse kuyembekeza mokhazikika mtima kudza kwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, December 6, 2025

LAMULUNGU LA 2 MU NYENGO YA ADVENT—A


LAMULUNGU LA 2 MU NYENGO YA ADVENT—A

“Konzani njira yodzeramo Ambuye.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA: YESAYA 11:1-10. (Amphawi adzawaweruza mwachilungamo).

 

Nthambi idzaphuka patsinde pa Yese, ndipo mphukira idzatuluka ku mizu yake. Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, Mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziwa zinthu ndi kuwopa Chauta. Ndipo kuopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva. Koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzawagamulira mlandu wawo mosakondera. Mau ochokera m’kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa. Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake, ndipo kukhulupirika, ngati chomangira m’chiwuno mwake. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang’ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng’ono nkumaziweta. Ng’ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana awo adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Mwana woyamwa adzasewera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipazakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzadza ndi nzeru ya kudziwa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi. Otengedwa ku ukapolo adzabwerako. Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72:1-2, 7-8, 12-13, 17.

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

 

Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,

Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,

Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,

Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula,

Mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

Idzakhala ikulamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina,

Kuchokeranso ku mtsinje mpaka ku mathero a dziko.

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

 

Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,

Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,

Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,

Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

 

Dzina lake lisaiwalike, mbiri yake ikhalepobe,

Monga momwe limakhalira dzuwa,

Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo,

A mitundu yonse aitche yodala.

 

Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!

-----------------------------------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA YOLEMBERA AROMA: AROMA 15:4-9. (Khristu ndi Mpulumutsi wa anthu onse).

 

Abale, zonse zolembedwa m’Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowa amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo. Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira nawalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe. Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adawalonjeza makolo ao akale aja, ndiponso pakutsata anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—LUKA 3:4, 6.

Alleluia, Alleluia!!—Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu—Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 3:1-12. (Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wa Mulungu wayandikira).

 

Pa masiku amenewo kudabwera Yohane M’batizi nayamba kulalika m’chipululu cha ku Yudeya. Ankati, “tembenukani mtima chifukwa Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.” Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adati, “Liwu la munthu wofuula m’chipululu; akunena kuti, ‘konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.” Yohane yo ankavala zovala za ubweya wangamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m’chiwuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wam’thengo. Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye. Ndiye ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumawabatiza mu Mtsinje wa Yordaniwo. Ankaona Ayuda ambiri a m’gulu la Afarisi ndi Asaduki akubwera kuti iye awabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthawe chilango cha Mulungu chikudzachi? Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m’mitima mwanu musayerekeze zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto. Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m’moto. Chopetera chake chili m’manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m’nkhokwe, koma mankhusu adzawatentha m’moto wosazimika.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu Khristu adadzera anthu a mafuko onse, tiyeni, ndi mtima umodzi, tiyamike Atate athu a Kumwamba ndi kupempha madalitso ao pa ife ndi pa anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti mau a m’Malembo Oyera alimbitse chikhulupiriro ndi chikondi m’mtima mwao pa nyengo ino ya Adventi.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere Ayuda, kuti Mulungu aunikire nzeru zawo mpaka kuti iwonso avomere Yesu Khristu Mpulumutsi, potsata zonse zija zidalembedwa m’Malembo Oyera.
Tikupemphani mutivomereze.

3.     Tipempherere anthu a mitundu yonse amene adakali padera, kuti maso ao atsekuke ndipo mitima yao ikopedwe ndi zitsanzo zokoma za akhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tipempherere ife tonse tili muno, kuti tilimbikire kudzetsa chilungamo ndi mtendere pakati pa anzathu, pakuwatumikira ndi mtima wachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mau anu akhazikike m’mitima mwathu, kuti moyo wathu uwonetse zipatso zokomera Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB


Saturday, November 29, 2025

LAMULUNGU LA 1 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 1 MU NYENGO YA ADVENT—A

“Tikhale okonzeka poyembekeza kudza kwa Ambuye.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA: YESAYA 2:1-5. (Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu a mitundu yambiri adzabwera).

Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya, mwana wa Amozi, adaziwona m’masomphenya. Pa masiku akudzawa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu amitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m’njira zakezo. Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo. Inu zidzukulu za Yakobe, tiyeni tiyende m’kuwala kwa Chauta.”

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 122:1-2, 4-5, 6-9.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.

 

Ndidasangala pamene adandiwuza kuti,

“Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta,”

Mapazi athu akhala akuima m’kati mwa zipata zako,

Iwe Yerusalemu.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.

 

Kumeneko kumapita mafuko onse, anthu ake a Chauta,

Monga momwe adzalamulira Israele,

Kuti ayamike dzina la Chauta,

Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira,

Mipando yake ya banja la Davide.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.

 

Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti,

“Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu,

Zinthu ziziwayendera bwino,

Mtendere ukhale m’kati mwa makoma ako,

Bata likhale m’nyumba zako zachifumu.”

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.

 

Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzanena kuti,

“Mtendere ukhaledi m’kati mwako.”

Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu,

Ndidzakupemphera zabwino.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.

-----------------------------------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA YOLEMBERA AROMA: AROMA 13:11-14. (Chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira).

Abale, mukudziwa kuti yafika kale nthawi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopanso kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo.

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—SALIMO 85:8.

Alleluia, Alleluia!!—Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 24:37-44. (Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Ambuye anu adzabwere).

 

Yesu anati kwa ophunzira ake: “kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthawi ya Nowa. Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adalowa m’chombo. Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuwaononga onse. Zidzateronso pamene mwana wa Munthu adzabwera. Pa nthawi imeneyo anthu awiri adzakhala ali m’munda, mmodzi adzamutenga, winayo nkumusiya. Azimai awiri adzakhala akusinja mmodzi adzamutenga, winayo nkumusiya. “Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziwani kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukuyembekeza.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, anthu ambiri adakali m’tulo, osazindikira kuti Ambuye akubwera. Tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba, kuti achotse mdima m’mitima yathu ndi ya anthu onse:

 

1.     Tipempherere Eklezia wa Mulungu, kuti aunikire anthu a mafuko onse ndi maphunzitso ake, awaonetse kuti Ambuye anadzakhaladi pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko aleke kukhulupirira zida zankhondo, ndipo alimbikire kukhazikitsa bata ndi mtendere pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto osiyanasiyana, apeze anthu a chifundo owathandiza m’zosowa zao, ndipo asaleke kukhulupirira Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno, mapemphero a nyengo ino ya Adventi atithandize kukometsa makhalidwe athu ndi kukula m’chikhulupiriro.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, okoma mtima, landirani mapemphero athuwa, pamodzi ndi mafuno ndi madandaulo a anthu onse amene akuyembekeza chithandizo chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, November 22, 2025

CHAKA CHA YESU KHRISTU MFUMU—LAMULUNGU LOTSIRIZA MU CHAKA CHA MPINGO—C

CHAKA CHA YESU KHRISTU MFUMU.

LAMULUNGU LOTSIRIZA MU CHAKA CHA MPINGO—C.

“Adatigawirako zokoma za Ufumu wake.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LACHIWIRI LA SAMUELE: 2 SAMUELE 5:1-3. (Adomdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse).

 

Pambuyo pake mafuko onse a Aisraele adadzasonkhona kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi. Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Israele.’” Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono mfumu Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 122:1-5.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti,

“Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta,”

Mapazi athu akhala akuima m’kati mwa zipata zako,

Iwe Yerusalemu.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”

 

Yerusalemu adamangidwa bwino,

Zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi,

Kumeneko kumapita mafuko onse,

Anthu ake a Chauta.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”

 

Monga momwe adzalamulira Israele,

Kuti akayamike dzina la Chauta,

Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira,

Mipando yake ya banja la Davide.

 

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”

-----------------------------------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE: AKOLOSE 1:12-20 (Iye anatilowetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa).

 

Abale, timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuwala. Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutilowetsa mu Ufumu wa mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu. Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye mwana wake Woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezi adalenga Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse padakalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—MARKO 11:9, 10.

Alleluia, Alleluia!!—Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye. Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. —Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 23: 35-43. (Ambuye, mukandikumbukire mukakafika mu Ufumu wanu).

 

Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera.  Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.” Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. Adati, “Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m’Chigriki, m’Chilatini, ndi m’Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.” Chigawenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.” Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziwirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma awa sadachite cholakwa chilichonse.” Ndipo adati, “Inu, mukandikumbukire mukakafika mu Ufumu wanu.” Yesu adamuyankha kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, kumwamba.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, popeza kuti ndife anthu ake a Yesu Khristu, tiyeni tonse pamodzi naye tipemphere kwa Mulungu, kuti Ufumu wake udze:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri a Mpingo, atumikire anthu awo modzichepetsa ndi modziiwala, potsatira Yesu Khristu, Mfumu ya mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu a mipingo yonse akondane ndi kumafunitsitsa kukhala amodzi m’chikhulupiriro monga adafunira Yesu Khristu, Mutu wake wa Mpingo.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akulu onse olamulira maiko alimbikire kukhazikitsa chilungamo ndi chimvano pakati pa anthu ao, kuti ponseponse pakhale mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino tikondane ndi kugwirizana mwa ubale kusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ulikukhazikikadi pakati pathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka mapemphero athuwa kwa Inu, tikukuyamikani mokondwa, chifukwa mwayamba kale kutigawira zokoma zimene mukutisungira mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A [Gaudete Sunday] “Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”   MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’N...